22“Diso ndi nyale ya thupi. Ngati maso ako ali bwino, thupi lako lonse lidzakhala mʼkuwala.
23Koma ngati maso ako sali bwino, thupi lako lonse lidzakhala mu mdima. Koma ngati kuwala kuli mwa iwe ndi mdima, ndiye kuti mdimawo ndi waukulu bwanji!
24“Palibe munthu angathe kukhala kapolo wa ambuye awiri. Pakuti pena adzamuda mmodzi ndi kukonda winayo kapena adzagwira ntchito mokhulupirika kwa mmodzi, nadzanyoza winayo. Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa chuma pa nthawi imodzi.
25“Nʼchifukwa chake ndikuwuzani kuti musadere nkhawa za moyo wanu kuti mudzadya chiyani kapena mudzamwa chiyani; kapenanso za thupi lanu kuti mudzavala chiyani. Kodi moyo suposa chakudya? Kodi thupi siliposa zovala?
27Kodi ndani wa inu podandaula angathe kuwonjeza ora limodzi pa moyo wake?
28“Ndipo bwanji inu mudera nkhawa za zovala? Onani makulidwe a maluwa akutchire. Sagwira ntchito kapena kuwomba nsalu.
29Ndikukuwuzani kuti angakhale Solomoni mu ulemerero wake sanavale mofanana ndi limodzi la maluwa amenewa.
30Ngati umu ndi mmene Mulungu avekera udzu wa kutchire umene ulipo lero ndipo mawa uponyedwa ku moto, kodi sadzakuvekani koposa? Aa! Inu a chikhulupiriro chochepa!
31Chifukwa chake musadere nkhawa ndi kuti, ‘Tidzadya chiyani?’ kapena ‘Tidzamwa chiyani?’ kapena ‘Tidzavala chiyani?’