1Iye atatsika ku phiri kuja, anthu ambirimbiri anamutsata.
2Ndipo munthu wakhate anadza kwa Yesu namugwadira nati, “Ambuye, ngati mufuna, mukhoza kundiyeretsa.”
3Yesu anatambasula dzanja lake namukhudza munthuyo nati,
4Ndipo Yesu anati kwa iye,
5Yesu atalowa mʼKaperenamu, Kenturiyo anabwera kwa Iye napempha chithandizo,
6nati, “Ambuye, wantchito wanga ali chigonere ku nyumba, sakuthanso kuyenda, akumva kuwawa kwambiri.”
7Ndipo Yesu anati kwa iye,
8Kenturiyo uja anayankha kuti, “Ambuye, ndine wosayenera kuti Inu mukalowe mʼnyumba mwanga. Koma mungonena mawu ndipo wantchito wanga adzachiritsidwa.
9Pakuti inenso ndili pansi pa ulamuliro ndipo ndili ndi asilikali amene ndiwalamulira. Ndikalamulira mmodzi kuti, ‘Pita,’ amapita; ndi kwa wina kuti, ‘Bwera,’ amabwera. Ndikawuza wantchito wanga kuti, ‘Chita ichi,’ iye amachita.”
10Yesu atamva zimenezi, anadabwa ndipo anati kwa omutsatira,
11
12
13Pamenepo Yesu anati kwa Kenturiyo,
14Ndipo Yesu atalowa mʼnyumba ya Petro, anaona mpongozi wake wa Petro ali gone akudwala malungo.
15Ndipo Yesu anakhudza dzanja lake ndipo pomwepo anachira nayamba kumutumikira.
16Itafika nthawi yamadzulo, anthu anabweretsa kwa Iye anthu ambiri ogwidwa ndi ziwanda ndipo anatulutsa ziwandazo ndi mawu okha, nachiritsa odwala onse.
17Uku kunali kukwaniritsa zimene ananena mneneri Yesaya kuti,
18Yesu ataona gulu la anthu litamuzungulira, analamula kuti awolokere kutsidya lina la nyanja.
19Ndipo mphunzitsi wa malamulo anabwera kwa Iye nati, “Aphunzitsi, ine ndidzakutsatani kulikonse kumene muzipita.”
20Yesu anayankha kuti,
21Wophunzira wina anati kwa Iye, “Ambuye, mundilole ndiyambe ndakayika maliro a abambo anga.”
22Koma Yesu anamuwuza kuti,
23Iye atalowa mʼbwato, ophunzira ake anamutsatira.
24Ndipo taonani mwadzidzidzi mphepo yayikulu yamkuntho inawomba pa nyanjapo, kotero kuti bwatolo linayamba kumizidwa ndi mafunde. Koma Yesu anali mtulo.
25Ophunzira ake anapita namudzutsa nati, “Ambuye! Tipulumutseni! Tikumira!”
26Iye anawayankha kuti,
27Ndipo ophunzirawo anadabwa nafunsa kuti, “Ndi munthu wotani uyu? Kuti ngakhale mphepo ndi mafunde zimvera Iye!”
28Ndipo atafika ku mbali ina ya dera la Gadara, anakumana ndi anthu awiri ogwidwa ndi ziwanda akuchokera ku manda. Iwowa anali woopsa kwambiri kotero kuti panalibe munthu akanatha kudzera njira imeneyo.
29Ndipo iwo anafuwulira kwa Yesu nati, “Mukufuna chiyani kwa ife, Inu Mwana wa Mulungu? Kodi mwabwera kuno kudzatizunza nthawi yake isanafike?”
30Ndipo patali pake panali gulu la nkhumba zimene zimadya.
31Ndipo ziwandazo zinamupempha Yesu kuti, “Ngati mutitulutsa ife mutitumize mu nkhumba izo.”
32Iye anati kwa ziwandazo,
33Koma amene amaziweta anathawa nalowa mʼmudzi nafotokoza zonse, kuphatikizapo zimene zinachitika ndi anthu ogwidwa ndi ziwanda aja.
34Ndipo anthu onse a mʼmudziwo anatuluka kukakumana ndi Yesu. Ndipo atamuona Iye, anamupempha kuti achoke mʼdera lawo.