Miyambo 1:1-33 NYCCL2016 - Bible AI

1Iyi ndi miyambi ya Solomoni mwana wa Davide, mfumu ya Israeli:

2Ndi yothandiza kuti munthu adziwe nzeru ndi malangizo; kuti amvetse mawu a matanthauzo ozama;

3kuti alandire malangizo othandiza kuti achite zinthu mwanzeru, akhale wangwiro, wachilungamo ndiponso wosakondera.

4Ndi yothandiza munthu wamba kuti aphunzire nzeru za kuchenjera, achinyamata kudziwa zinthu bwino ndi kulingalira.

5Munthu wanzeru amvetse bwino miyamboyi kuti awonjezere kuphunzira kwake, ndi munthu womvetsa zinthu bwino apatepo luso,

6kuti azimvetsa miyambi ndi mafanizo, mawu a anthu anzeru ndi mikuluwiko.

6

7Kuopa Yehova ndiye chiyambi cha nzeru. Zitsiru zimanyoza nzeru ndi malangizo.

8Mwana wanga, mvera malangizo a abambo ako ndipo usakane mawu okuwongolera a amayi ako.

9Ali ngati sangamutu yokongola ya maluwa pamutu pako ndiponso ali ngati mkanda mʼkhosi mwako.

9

10Mwana wanga, ngati anthu oyipa afuna kukukopa usamawamvere.

11Akadzati, “Tiye kuno; tikabisale kuti tiphe anthu, tikabisalire anthu osalakwa;

12tiwameze amoyo ngati manda, ndi athunthu ngati anthu otsikira mʼdzenje.

13Motero tidzapeza zinthu zosiyanasiyana zamtengowapatali ndi kudzaza nyumba zathu ndi zolanda;

14Bwera, chita nafe maere, ndipo tidzagawana chuma chathu tonse.”

15Mwana wanga, usayende nawo pamodzi, usatsagane nawo mʼnjira zawozo.

16Iwowatu amangofuna zoyipa zokhazokha, amathamangira kukhetsa magazi.

17Nʼkopanda phindu kutchera msampha mbalame zikuona!

18Koma anthu amenewa amangobisalira miyoyo yawo yomwe; amangodzitchera okha msampha!

19Awa ndiwo mathero a anthu opeza chuma mwankhanza; chumacho chimapha mwiniwake.

20Nzeru ikufuwula mu msewu, ikuyankhula mokweza mawu mʼmisika;

21ikufuwula pa mphambano ya misewu, ikuyankhula pa zipata za mzinda kuti,

21

22“Kodi inu anthu osachangamukanu, mudzakondwera ndi kusachangamuka mpaka liti? Nanga anthu onyogodola adzakondabe kunyogodola mpaka liti? Kapena opusa adzadana ndi nzeru mpaka liti?

23Tamverani mawu anga a chidzudzulo. Ine ndikukuwuzani maganizo anga ndi kukudziwitsani mawu anga.

24Popeza ndinakuyitanani koma inu munakana kumvera. Ndinayesa kukuthandizani koma panalibe amene anasamala.

25Uphungu wanga munawunyoza. Kudzudzula kwanga simunakusamale.

26Ndiye inenso ndidzakusekani mukadzakhala mʼmavuto; ndidzakunyogodolani chikadzakugwerani chimene mumachiopacho.

27Chiwonongeko chikadzakugwerani ngati namondwe, tsoka likadzakufikirani ngati kamvuluvulu, mavuto ndi masautso akadzakugwerani.

27

28“Tsono mudzandiyitana koma sindidzayankha; mudzandifunafuna, koma simudzandipeza.

29Popeza iwo anadana ndi chidziwitso ndipo sanasankhe kuopa Yehova,

30popeza iwo sanasamale malangizo anga ndipo ananyoza chidzudzulo changa.

31Tsono adzadya zipatso zoyenera mayendedwe awo ndi kukhuta ndi ntchito zimene anachita kwa ena.

32Pakuti anthu osachangamuka amaphedwa chifukwa cha kusochera kwawo, ndipo zitsiru zimadziwononga zokha chifukwa cha mphwayi zawo.

33Koma aliyense wondimvera adzakhala mwa bata; adzakhala mosatekeseka posaopa chilichonse.”