1Ponya chakudya chako pa madzi,udzachipezanso patapita masiku ambiri.
2Ndalama zako uzisungitse kwa anthu asanu ndi awiri, inde kwa anthu asanu ndi atatu,pakuti sudziwa ndi tsoka lanji limene likubwera pa dziko.
2
3Ngati mitambo yadzaza ndi madzi,imagwetsa mvula pa dziko lapansi.Mtengo ukagwera cha kummwera kapena cha kumpoto,ndiye kuti udzagonera kumene wagwerako.
5Momwe sudziwira mayendedwe a mphepo,kapena momwe mzimu umalowera mʼthupi la mwana mʼmimba mwa amayi,momwemonso sungathe kudziwa ntchito za Mulungu,Mlengi wa zinthu zonse.
7Kuwala nʼkwabwino,ndipo maso amasangalala kuona dzuwa.
8Munthu akakhala wa zaka zambiri,mulekeni akondwerere zaka zonsezo,koma iye azikumbukira masiku a mdima,pakuti adzakhala ochuluka.Chilichonse chimene chikubwera ndi chopanda phindu.
8
9Kondwera mnyamata iwe, pamene ukanali wamngʼono,ndipo mtima wako usangalale pa nthawi ya unyamata wako.Tsatira zimene mtima wako ukufuna,ndiponso zimene maso ako akuona,koma dziwa kuti pa zinthu zonsezoMulungu adzakuweruza.
10Choncho uchotse zokusautsa mu mtima mwako,upewe zokupweteka mʼthupi mwako,pakuti unyamata ndi ubwana ndi zopandapake.