2Nthawi ya ukalamba wako, dzuwa ndi kuwala,mwezi ndi nyenyezi zidzada.Mitambo idzabweranso mvula itagwa.
3Nthawi imene manja ako adzanjenjemera,miyendo yako idzafowoka,pamene mano ako adzalephera kutafuna chifukwa ndi owerengeka,ndipo maso ako adzayamba kuchita chidima.
4Makutu ako adzatsekeka,ndipo sudzamva phokoso lakunja;sudzamvanso kusinja kwa pa mtondokapena kulira kwa mbalame mmawa.
5Imeneyi ndiyo nthawi imene anthu amaopa kupita kumalo okwera,amaopa kuyenda mʼmisewu;Mutu umatuwa kuti mbuu,amayenda modzikoka ngati ziwalandipo chilakolako chimatheratu.Nthawi imeneyo munthu amapita ku nyumba yake yamuyayandipo anthu olira maliro amayendayenda mʼmisewu.
5
6Kumbukira Iye chingwe cha siliva chisanaduke,kapena mbale yagolide isanasweke;mtsuko usanasweke ku kasupe,kapena mkombero usanathyoke ku chitsime.
7Iyi ndi nthawi imene thupi lidzabwerera ku dothi, kumene linachokera,mzimu udzabwerera kwa Mulungu amene anawupereka.
7
8“Zopanda phindu! Zopandapake!” akutero Mlaliki.“Zonse ndi zopandapake!”
9Mlaliki sanali wozindikira zinthu kokha ayi, komanso ankaphunzitsa anthu. Iye ankasinkhasinkha ndi kufufuzafufuza ndi kulemba mwadongosolo miyambi yambiri.