1Uthenga wonena za Ninive. Buku la masomphenya a Nahumu wa ku Elikosi.
2Yehova ndi Mulungu wansanjendiponso wobwezera;Yehova amabwezera ndipo ndi waukali.Yehova amabwezera adani akendipo ukali wake umakhala nthawi zonse pa adani akewo.
3Yehova sakwiya msanga koma ndi wa mphamvu yayikulu;ndipo sadzalola kuti munthuwolakwa asalangidwe.Iye amayenda mʼkamvuluvulu ndi mʼnamondwe,ndipo mitambo ndi fumbi la ku mapazi ake.
4Amalamulira nyanja ndipo imawuma;amawumitsa mitsinje yonse.Zomera za ku Basani ndi Karimeli zimawumandipo maluwa a ku Lebanoni amafota.
12Yehova akuti,“Ngakhale Asiriyawo ali ndi abwenzi,kaya iwowo ndi ambiri,koma adzawonongedwa ndi kutheratu.Ngakhale ndinakuzunza iwe Yuda,sindidzakuzunzanso.
13Tsopano ndidzathyola goli lake pa khosi lakondipo ndidzadula maunyolo ako.”
13
14Yehova walamulira za iwe, Ninive kuti,“Sudzakhala ndi zidzukuluzimene zidzadziwike ndi dzina lako.Ndidzawononga zifanizo zosema ndi mafano owumbaamene ali mʼnyumba ya milungu yako.Ine ndidzakukumbira mandachifukwa ndiwe woyipitsitsa.”
15Taonani, pa phiripo,mapazi a munthu amene akubweretsa nkhani yabwino,amene akulengeza za mtendere!Inu anthu a ku Yuda, chitani madyerero anundipo kwaniritsani malumbiro anu.Anthu oyipa sadzakuthiraninso nkhondo;iwo adzawonongedwa kotheratu.