12Balaamu anayankha Balaki kuti, “Kodi sindinawawuze amithenga amene munawatumiza kwa ine,
13kuti ngakhale Balaki atandipatsa nyumba yake yaufumu yodzaza ndi siliva ndi golide sindingathe kuchita zinthu mwa ine ndekha, zabwino kapena zoyipa, kuposa lamulo la Yehova ndi kuti ndiyenera kunena zokhazo zimene Yehova akunena?
14Tsopano ndikupita kwa anthu anga, koma tabwerani ndikuchenjezeni zimene anthu awa adzachitira anthu anu masiku akubwerawa.”
15Ndipo iye ananena uthenga wake nati, “Uthenga wa Balaamu mwana wa Beori,uthenga wa amene diso lake ndi lotsekuka.
16Uthenga wa amene amamva mawu a Mulungu,amene ali ndi nzeru zochokera kwa Wammwambamwamba,amene amaona masomphenya wochokera kwa Wamphamvuzonse,amene amagwa chafufumimba koma diso lake lili lotsekuka:
16
17“Ndikumuona iye koma osati tsopano;ndikumupenya iye koma osati pafupi.Nyenyezi idzatuluka mwa Yakobo;ndodo yaufumu idzatuluka mwa Israeli.Iye adzagonjetsa Mowabundi kugonjetsa ana onse a Seti.
18Edomu adzagonjetsedwa;Seiri, mdani wake, adzawonongedwakoma mphamvu za Israeli zidzachuluka.
19Wolamulira adzachokera mwa Yakobondipo adzawononga otsala a mu mzindamo.”
20Kenaka Balaamu anaona Aamaleki ndipo ananena uthenga wake uwu: “Aamaleki anali oyamba mwa mitundu ya anthukoma potsiriza pake adzawonongeka.”
21Kenaka anaonanso Akeni ndipo ananena uthenga wake, “Malo amene mukukhalamo ndi otetezedwa,chisa chanu chinayikidwa pa thanthwe;