1Utatha mliri Yehova anati kwa Mose ndi Eliezara mwana wa Aaroni,
2“Werengani Aisraeli onse mwa mabanja awo, onse a zaka makumi awiri kapena kuposera pamenepo omwe angathe kugwira ntchito ya usilikali mʼgulu lankhondo la Israeli.”
3Kotero mu zigwa za Mowabu pafupi ndi mtsinje wa Yorodani ku Yeriko, Mose ndi wansembe Eliezara anayankhula nawo kuti,
4“Werengani amuna a zaka makumi awiri kapena kuposera pamenepo, monga momwe Yehova walamulira Mose.”
5Zidzukulu za Rubeni, mwana woyamba wamwamuna wa Israeli, zinali izi:
6
7Awa anali mafuko a Rubeni: onse amene anawerengedwa analipo 43,730.
8Mwana wa Palu anali Eliabu,
9ndipo ana a Eliabu anali Nemueli, Datani ndi Abiramu. Datani ndi Abiramu anali gulu la akuluakulu aja amene anawukira Mose ndi Aaroni ndipo analinso mʼgulu la otsatira Kora pamene anawukira Yehova.
10Nthaka inangʼambika ndi kuwameza pamodzi ndi Kora, kotero kuti gulu lawo linafa pamene moto unapsereza anthu 250 aja, nasanduka chenjezo.
11Koma ana a Kora sanafe nawo.
12Zidzukulu za Simeoni mwa mafuko awo zinali izi:
13
14Awa anali mafuko a Simeoni. Iwowa analipo amuna 22,200.
15Zidzukulu za Gadi mwa mafuko awo ndi izi:
16
17
18Awa ndiwo anali mafuko a Gadi. Onse amene anawerengedwa analipo 40,500.
19Eri ndi Onani anali ana aamuna a Yuda, koma anafera mu Kanaani.
20Zidzukulu za Yuda monga mwa mafuko awo zinali izi:
21
22Awa ndiwo anali mafuko a Yuda. Amene anawerenga analipo 76,500.
23Zidzukulu za Isakara monga mwa mafuko awo zinali izi:
24
25Awa ndi amene anali a fuko la Isakara. Amene anawerengedwa analipo 64,300.
26Zidzukulu za Zebuloni mwa mafuko awo zinali izi:
27Awa ndiwo anali mafuko a Zebuloni. Amene anawerengedwa analipo 60,500.
28Zidzukulu za Yosefe mwa mafuko awo kupyolera mwa Manase ndi Efereimu zinali izi:
29Zidzukulu za Manase:
30
31
32
33
34Awa ndiwo anali mafuko a Manase. Amene anawerengedwa analipo 52,700.
35Zidzukulu za Efereimu monga mwa mafuko awo zinali izi;
36
37Awa ndiwo anali mafuko a Efereimu. Amene anawerengedwa analipo 32,500.
38Zidzukulu za Benjamini monga mwa mabanja awo zinali izi:
39
40
41Awa ndiwo anali mabanja a Benjamini. Amene nawerengedwa analipo 45,600.
42Zidzukulu za Dani mwa mabanja awo zinali izi:
43Onse a fuko la Asuhamu amene anawerengedwa analipo 64,400.
44Zidzukulu za Aseri monga mwa mafuko awo zinali izi:
45
46
47Awa ndiwo anali mafuko a Aseri. Onse amene anawerengedwa analipo 53,400.
48Zidzukulu za Nafutali mwa mafuko awo zinali izi:
49
50Awa ndiwo anali mafuko a Nafutali. Onse amene anawerengedwa analipo 45,400.
51Chiwerengero chonse cha amuna mu Israeli chinalipo 601,730.
52Yehova anawuza Mose kuti,
53“Uwagawire dziko anthu awa kuti likhale cholowa chawo molingana ndi chiwerengero cha mayina awo.
54Gulu lalikulu ulipatse cholowa chachikulu, ndipo lochepa cholowa chocheperapo. Gulu lililonse lilandire cholowa chake molingana ndi chiwerengero cha amene anawerengedwa.
55Dzikolo uligawe pochita maere. Alandire cholowa chawocho potsata mayina a mafuko a makolo awo.
56Cholowa chawo uchigawe pakati pa fuko lalikulu ndi lalingʼono mwa maere.”
57Alevi omwe anawerengedwa monga mwa mafuko awo ndi awa:
58Awanso anali mabanja a Alevi:
59
60
61
62Alevi onse aamuna a mwezi umodzi kapena kuposera pamenepa analipo 23,000. Iwowo sanawerengedwe pamodzi ndi Aisraeli ena chifukwa sanalandire cholowa pakati pawo.
63Awa ndi amene anawerengedwa ndi Mose ndi Eliezara wansembe pamene ankawerenga Aisraeli pa zigwa za ku Mowabu mʼmbali mwa Yorodani ku Yeriko.
64Mwa anthu amenewa panalibe ndi mmodzi yemwe amene anali mʼgulu la Aisraeli omwe Mose ndi wansembe Aaroni anawawerenga mʼchipululu cha Sinai;
65Chifukwa Yehova anali atawuza Aisraeliwo kuti adzafera ndithu mʼchipululu, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene anatsala kupatula Kalebe mwana wa Yefune ndi Yoswa mwana wa Nuni.