1Masomphenya a Obadiya. Ambuye Yehova akunena kwa Edomu kuti, Tamva uthenga wochokera kwa Yehova:Nthumwi yatumidwa kupita kwa anthu a mitundu kukanena kuti,“Konzekani, tiyeni tikachite nkhondo ndi Edomu.”
2“Taona, ndidzakuchepetsani pakati pa anthu a mitundu ina;udzanyozedwa kwambiri.
3Kudzikuza kwa mtima wako kwakusocheretsa,iwe amene umakhala mʼmapanga a mʼmatanthwendipo umamanga nyumba zako pa mapiri ataliatali,iwe amene umanena mu mtima mwako kuti,‘Ndani anganditsitse pansi?’
6Koma Esau adzalandidwa zinthu zonse,chuma chake chobisika chidzabedwa!
7Anthu onse ogwirizana nawo adzakupirikitsira kumalire;abwenzi ako adzakunyenga ndi kukugonjetsa;amene amadya chakudya chako adzakutchera msampha,koma iwe sudzazindikira zimenezi.”
7
8Yehova akunena kuti, “Tsiku limenelo,kodi sindidzawononga anthu onse anzeru a ku Edomu,anthu odziwa zinthu mʼmapiri a Esau?
9Ankhondo ako, iwe Temani, adzachita mantha,ndipo aliyense amene ali mʼphiri la Esauadzaphedwa pa nkhondo.
10Chifukwa cha nkhanza zimene unachitira mʼbale wako Yakobo,udzakhala wamanyazi;adzakuwononga mpaka muyaya.
11Pamene adaniankamulanda chuma chakepamene alendo analowa pa zipata zakendi kuchita maere pa Yerusalemu,pa tsikulo iwe unali ngati mmodzi wa iwo.
12Iwe sunayenera kunyoza mʼbale wakopa nthawi ya tsoka lake,kapena kunyogodola Ayudachifukwa cha chiwonongeko chawo,kapena kuwaseka pa nthawi yamavuto awo.
13Iwe sunayenera kudutsa pa zipata za anthu angapa nthawi ya masautso awo,kapena kuwanyogodolapa tsiku la tsoka lawo,kapena kulanda chuma chawopa nthawi ya masautso awo.
14Sunayenera kudikirira pamphambano ya misewukuti uphe Ayuda othawa,kapena kuwapereka kwa adani awo Ayuda opulumukapa nthawi ya mavuto awo.”
14
15“Tsiku la Yehova layandikiralimene adzaweruza mitundu yonse ya anthu.Adzakuchitira zomwe unawachitira ena;zochita zako zidzakubwerera wekha.
16Iwe unamwa pa phiri langa loyera,koteronso mitundu ina yonse idzamwa kosalekeza;iwo adzamwa ndi kudzandirandipo adzayiwalika pa mbiri ya dziko lapansi.
17Koma pa Phiri la Ziyoni padzakhala chipulumutso;phirilo lidzakhala lopatulika,ndipo nyumba ya Yakoboidzalandira cholowa chake.
18Nyumba ya Yakobo idzasanduka motondipo nyumba ya Yosefe idzasanduka lawi la moto;nyumba ya Esau idzasanduka chiputu,ndipo adzayitenthe pa moto ndi kuyipsereza.Sipadzakhala anthu opulumukakuchokera mʼnyumba ya Esau.”Yehova wayankhula.
18
19Anthu ochokera ku Negevi adzakhalaku mapiri a Esau,ndipo anthu ochokera mʼmbali mwa mapiriadzatenga dziko la Afilisti.Adzakhala mʼminda ya Efereimu ndi Samariya,ndipo Benjamini adzatenga Giliyadi.
20Aisraeli amene ali ku ukapoloadzalandira dziko la Kanaani mpaka ku Zarefati;a ku Yerusalemu amene ali ku ukapolo ku Sefaradiadzalandira mizinda ya ku Negevi.
21Opulumukawo adzapita ku Phiri la Ziyonindipo adzalamulira mapiri a Esau.Koma ufumuwo udzakhala wa Yehova.