2Inu munawadzala ndipo anamera mizu;amakula ndi kubereka zipatso.Dzina lanu limakhala pakamwa pawo nthawi zonse,koma mitima yawo imakhala kutali ndi Inu.
3Koma Inu Yehova, ine mumandidziwa;mumandiona ndipo mumayesa zolingalira zanga.Akokeni anthu oyipawo ngati nkhosa zokaphedwa!Ayikeni padera mpaka tsiku loti akaphedwe!
4Kodi dziko lidzakhala likulirabe mpaka litindipo udzu mʼmunda uliwonse udzakhalabe ofota mpaka liti?Nyama ndi mbalame kulibiretuchifukwa anthu amene amakhalamo ndi oyipa.Iwo amati:“Yehova sangathe kuona ntchito zathu.”
5Yehova anayankha kuti, “Ngati kukutopetsa kuthamanga pamodzi ndi anthunanga ungapikisane bwanji ndi akavalo?Ngati ukupunthwa ndi kugwa pa malo abwino,udzatha bwanji kuthamanga mʼnkhalangoza ku Yorodani?
12Anthu onse owononga abalalikiraku zitunda zonse za mʼchipululu.Yehova watuma ankhondo akekudzawatha kuyambira kumalire ena a dziko mpaka ku malire enanso a dziko,ndipo palibe amene adzakhale pa mtendere.
13Anthu anafesa tirigu koma anatuta minga;anadzitopetsa kugwira ntchito koma osapeza phindu lililonse.Choncho mudzachita manyazi ndi zokolola zanuchifukwa cha mkwiyo wa Yehova.”
14“Anthu oyipa oyandikana ndi anthu anga Aisraeli, akuwalanda Aisraeliwo dziko, cholowa chimene ndinawapatsa. Nʼchifukwa chake ndidzawachotsa mʼdziko limenelo, ndipo ndidzachotsa banja la Yuda pakati pawo.
15Komabe nditawachotsa, ndidzawachitiranso chifundo, ndipo ndidzabwezera aliyense cholowa chake ndi dziko lake.
16Ndipo ngati iwo adzaphunzira bwino njira za anthu anga ndi kulumbira mʼdzina langa, namanena kuti, ‘Pali Yehova wamoyo,’ monga iwo anaphunzitsira anthu anga kulumbira mʼdzina la Baala, Ine ndidzawakhazikitsa pakati pa anthu anga.
17Koma ngati mtundu wina uliwonse sudzamvera, Ine ndidzawuchotsa ndi kuwuwonongeratu,” akutero Yehova.