2“ ‘Oyenera kufa adzafa;oyenera kufa ndi lupanga adzafa ndi lupanga;oyenera kufa ndi njala adzafa ndi njala;oyenera kupita ku ukapolo adzapita ku ukapolo.’
4Ndidzawasandutsa kukhala chinthu chonyansa kwa anthu a maufumu onse a dziko lapansi chifukwa cha zimene Manase mwana wa Hezekiya mfumu ya Yuda anachita mu Yerusalemu.
5“Kodi adzakumvera chisoni ndani, Yerusalemu?Kodi adzakulira ndani?Kodi ndani amene adzapatuka kufunsa za moyo wako?
6Inu mwandikana Ine,” akutero Yehova.“Inu mukubwererabe mʼmbuyo.Choncho Ine ndidzakukanthani.Ndatopa ndi kukuchitirani chifundo.
7Ine ndidzakubalalitsani kukuchotsani mʼmizinda ya mʼdzikomomonga mmene amachitira ndi mankhusu popeta ndi lichero.Anthu anga ndinawaliritsa ndi kuwawonongachifukwa sanasinthe makhalidwe awo oyipa.
8Ndinachulukitsa amayi awo amasiyekupambana mchenga wa kunyanja.Amayiwo ndinawawonongera ana awo aamunadzuwa lili pamutu.Mwadzidzidzi ndinawagwetserakuwawa mtima ndi mantha.
9Mayi wa ana asanu ndi awiri wakomokandipo akupuma wefuwefu.Dzuwa lake lalowa ukanali usana;anamuchititsa manyazi ndipo wathedwa nzeru.Otsala ndidzawapereka mʼmanja mwa adani awokuti awaphe ndi lupanga,”akutero Yehova.
9
10Kalanga ine, amayi pakuti munandibereka ine,munthu amene ndikutsutsana ndi kulimbana ndi anthu pa dziko lonse!Ine sindinakongoze kapena kukongola kanthu,komatu aliyense akunditemberera.
11Yehova anati, “Ndithudi, Ine ndidzakulanditsa kuti upeze bwino.Ndithudi, adani ako adzakupempha pa nthawi ya tsokandi ya mavuto awo.
15Ine ndinati, “Inu Yehova, mumadziwa zonse;kumbukireni ndi kundisamalira.Ndilipsireni anthu ondizunza.Ndilezereni mtima musandilande moyo wanga.Onani momwe ndi kuvutikira chifukwa cha Inu.
16Munandiyankhula ndipo mawu anu ndinawalandira bwino.Mawu anu anandipatsa chimwemwe ndipo mtima wanga unasangalala.Paja ine, Yehova Mulungu Wamphamvuzonse,ndimadziwika ndi dzina lanu.
17Sindinakhale nawo mʼgulu la anthu amadyera,sindinasangalale nawo anthu amenewo.Ndinakhala ndekha chifukwa choti dzanja lanu linali pa inendipo munadzaza mu mtima mwanga ndi mkwiyo.