15Adani ake abangulirandi kumuopseza ngati mikango.Dziko lake analisandutsa bwinja;mizinda yake anayitentha popanda wokhalamo.
16Ndiponso Aigupto a ku Mefisi ndi a ku Tapanesiakuphwanyani mitu.
17Zimenezitu zakuchitikiranichifukwa munasiya Yehova Mulungu wanupamene Iye ankakutsogolerani pa njira yanu?
18Tsopano mudzapindula chiyani mukapita ku Igupto,kukamwa madzi a mu Sihori?Ndipo mudzapindulanji mukapita ku Asiriya,kukamwa madzi a mu mtsinje wa Yufurate?
19Kuyipa kwanuko kudzakulangani;kubwerera mʼmbuyo kwanuko kudzakutsutsani.Tsono ganizirani bwino,popeza ndi chinthu choyipakundisiya Ine Yehova Mulungu wanu;ndi chinthu chowawa ndithu kusandiopa Ine Mulungu wanu.Akutero Ambuye Yehova Wamphamvuzonse.
19
20“Kuyambira kalekale inu munathyola goli lanundi kudula msinga zanu;munanena kuti, ‘Sitidzakutumikirani!’Ndithudi, inu mwakhala ngati mkazi wachiwerewere.Mukupembedza milungu ina pa phiri lililonse lalitalindiponso pansi pa mtengo uliwonse wa masamba ambiri.
21Ine ndinakudzala iwe ngati mtengo wampesa wosankhika;unali mpesa wabwino kwambiri ndi wodalirika.Nanga nʼchifukwa chiyani wasanduka mpesawachabechabe wonga wa kutchire?
22Ngakhale utasamba ndi sodakapena kusambira sopo wambiri,kuthimbirira kwa machimo ako kumaonekabe pamaso panga,”akutero Ambuye Yehova.
26“Monga momwe mbala imachitira manyazi pamene yagwidwa,moteronso nyumba ya Israeli idzachita manyazi;Aisraeliwo, mafumu ndi akuluakulu awo,ansembe ndi aneneri awo.
31“Inu anthu a mʼbado uno, ganizirani bwino mawu a Yehova: “Kodi Ine ndinakhalapo ngati chipululu kwa Israelikapena ngati dziko la mdima wandiweyani?Chifukwa chiyani anthu anga akunena kuti, ‘Ife tili ndi ufulu omayendayenda;sitidzabweranso kwa Inu’?
32Kodi namwali amayiwala zokongoletsera zake,kapena kuyiwala zovala zake za ukwati?Komatu anthu anga andiyiwalamasiku osawerengeka.