1Wansembe Pasuri mwana wa Imeri, woyangʼanira wamkulu wa Nyumba ya Yehova, anamva Yeremiya akulosera zinthu zimenezi.
2Tsono iye analamula kuti mneneri Yeremiyayo amenyedwe ndi kuyikidwa mʼndende pa Chipata chakumtunda kwa Benjamini ku Nyumba ya Yehova.
3Mmawa mwake, Pasuri anatulutsa Yeremiya mʼndende, ndipo Yeremiyayo anamuwuza kuti, “Pasuri, Yehova sadzakutchulanso dzina lako kuti Pasuri koma Zoopsa pa Mbali Zonse.
4Pakuti Yehova akuti, ‘Ndidzakusandutsa choopsa kwa mwiniwakewe ndi kwa abwenzi ako onse; iweyo ukuona. Anthu a ku Yuda ndidzawapereka onse mʼmanja mwa mfumu ya ku Babuloni. Ena adzatengedwa ukapolo ku Babuloni ndipo ena adzaphedwa pa nkhondo.
5Ndidzapereka kwa adani awo chuma chonse cha mu mzinda uno, phindu lonse la ntchito yake, zinthu zake zonse za mtengowapatali ndiponso katundu yense wa mafumu a ku Yuda. Iwo adzazitenga monga zinthu zolanda ku nkhondo ndi kupita nazo ku Babuloni.
6Ndipo iwe, Pasuri, pamodzi ndi onse a pa banja pako mudzapita ku ukapolo ku Babuloni. Mudzafera kumeneko ndi kuyikidwa mʼmanda, iweyo pamodzi ndi abwenzi ako amene unawalosera zabodza.’ ”
7Inu Yehova, mwandinamiza, ndipo ndinapusadi;Inu ndi wamphamvu kuposa ine ndipo munandipambana.Anthu akundinyoza tsiku lonse.Aliyense akundiseka kosalekeza.