1“Ngati munthu asudzula mkazi wakendipo mkaziyo nʼkuchoka nakakwatiwa ndi mwamuna wina,kodi mwamuna woyambayo angathe kumutenganso mkaziyo?Kodi atatero sindiye kuti dzikolo layipitsidwa kwambiri?Koma iwe Israeli wachita zadama ndi zibwenzi zambiri.Komabe bwerera kwa ine,”akutero Yehova.
2“Tayangʼana ku zitunda zowuma.Kodi aliponso malo ena amene iwe sunachitepo zadama?Iwe unkakhala mʼmbali mwa njira kumadikira zibwenzi zako,ngati Mluya wobisalira anthu mʼchipululu.Inu mwayipitsa dziko ndi zadama zanundi ntchito zanu zoyipa.
3Nʼchifukwa chake Yehova wayimitsa mvula,ndipo mvula ya nthawi ya masika sinagwe.Komabe uli ndi maonekedwe a mkazi wachiwerewere;ndipo sukuchita manyazi ndi pangʼono pomwe.
4Kodi iwe siposachedwa pomwepa pamene wanenakuti, ‘Abambo anga, Inu bwenzi langa la unyamata wanga,
14“Bwererani, ana osakhulupirika, pakuti ndine mbuye wanu,” akutero Yehova. “Ndinakusankhani, mmodzimmodzi kuchokera ku mudzi uliwonse ndiponso awiriawiri kuchokera ku banja lililonse.
15Ndipo ndidzakupatsani abusa a pamtima panga amene adzakutsogolerani mwanzeru ndi mwaluntha.
16Masiku amenewo mukadzachulukana kwambiri mʼdzikomo, anthu sadzanenanso za ‘Bokosi la Chipangano la Yehova’ kapena kuliganizira. Sadzalikumbukiranso kapena kulifuna, ndipo sadzapanganso lina,”
16akutero Yehova.
17Nthawi imeneyo adzatcha Yerusalemu Mpando Waufumu wa Yehova, ndipo mitundu yonse ya anthu idzasonkhana mu Yerusalemu pamaso pa Yehova. Sadzawumiriranso kutsata mitima yawo yoyipa.
18Masiku amenewo fuko la Yuda lidzaphatikizana ndi fuko la Israeli, onse pamodzi adzachokera ku dziko la kumpoto kupita ku dziko limene ndinapatsa makolo awo, kuti likhale cholowa.
19“Ine mwini ndinati, “ ‘Ndikanakonda bwanji kukukhazikani pakati pa ana angandikukupatsani dziko labwino kwambiri,cholowa chokongola kwambiri kuposa cha mitundu ina ya anthu.’Ndinaganiza kuti mudzanditcha Ine ‘Atate’ndi kuti simudzaleka kunditsata.
20Koma monga mkazi wosakhulupirika amasiya mwamuna wake,momwemonso inu mwakhala osakhulupirika kwa Ine, inu fuko la Israeli,”akutero Yehova.
20
21Mawu akumveka pa magomo,Aisraeli akulira ndi kupempha chifundochifukwa anatsata njira zoyipandi kuyiwala Yehova Mulungu wawo.