3Nthawi ikubwera pamene ndidzachotse anthu anga, Israeli ndi Yuda kuchokera ku ukapolo ndi kuwabwezera dziko limene ndinapatsa makolo awo,’ akutero Yehova.”
4Nawa mawu amene Yehova anayankhula ndi anthu a ku Israeli ndi Yuda:
5“Yehova akuti:
5“Ndamva kulira chifukwa cha nkhawa,ndamva kulira kwa mantha popeza palibe mtendere.
6Tsono khalani pansi ndi kudzifunsa kuti:Kodi munthu wamwamuna angathe kubereka mwana?Nanga nʼchifukwa chiyani ndikuona munthu aliyense wamwamunaatagwira manja ake pa mimba pake ngati mayi pa nthawi yake yochira?Chifukwa chiyani nkhope iliyonse ili yakugwa?
7Mayo ine! Tsiku limeneli ndi lalikulu kwambiri!Sipadzakhala lina lofanana nalo.Idzakhala nthawi ya masautso kwa Yakobo,koma adzapulumuka ku masautsowo.”
7
8Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Pa tsiku limenelo,ndidzathyola goli la ukapolo mʼkhosi mwawondipo ndidzadula zingwe zowamanga;Aisraeli sadzakhalanso akapolo a alendo.
14Abwenzi anu onse akuyiwalani;sasamalanso za inu.Ndakukanthani ngati mmene mdani akanachitira.Ndipo ndakulangani mwa nkhanza,chifukwa machimo anu ndi ambiri,ndipo kulakwa kwanu ndi kwakukulu.
15Chifukwa chiyani mukulira nacho chilonda chanu?Bala lanu silingapole ayi.Ine ndakuchitani zimenezi chifukwa machimo anu ndi ambirindipo kulakwa kwanu nʼkwakukulu.
17Ndidzachiza matenda anundi kupoletsa zilonda zanu,akutero Yehova,‘chifukwa mukutchedwa anthu otayika.Amati, ndi anthu a ku Ziyoni awa amene alibe wowasamala.’ ”
18Yehova akuti, “Ndidzabwera nalo banja la Yakobo ku dziko lawondipo ndidzachitira chifundo malo ake okhalamo;mzinda wa Yerusalemu udzamangidwanso pa bwinja pake,nyumba yaufumu idzamangidwanso pa malo pake penipeni.