5Mudzalimanso minda ya mpesapa mapiri a Samariya;alimi adzadzala mphesandipo adzadya zipatso zake.
6Lidzafika tsiku pamene alonda adzafuwulapa mapiri a Efereimu nati,‘Tiyeni tipite ku Ziyoni,kwa Yehova Mulungu wathu.’ ”
7Yehova akuti, “Imbani mosangalala chifukwa cha Yakobo,fuwulani chifukwa cha mtundu wopambana mitundu yonse.Matamando anu amveke, ndipo munene kuti,‘Yehova wapulumutsa anthu akeotsala a Israeli.’
8Taonani, ndidzabwera nawo kuchokera ku dziko la kumpoto,ndidzawasonkhanitsa kuchokera ku malekezero a dziko lapansi.Anthu osaona, olumala, amayi oyembekezerandi amene ali pa nthawi yawo yochira adzabwera nawo pamodzi.Chidzakhala chikhamu cha anthu obwerera kuno.
9Adzabwera akulira;koma Ine ndikuwatonthoza mtima, ndidzawaperekeza.Ndidzawatsogolera ku mitsinje yamadzimʼnjira yosalala mmene sadzapunthwamo.Chifukwa ndine abambo ake a Israeli,ndipo Efereimu ndi mwana wanga woyamba.
9
10“Imvani mawu a Yehova inu anthu a mitundu ina;lalikirani mawuwa kwa anthu a mayiko akutali a mʼmbali mwa nyanja;‘Iye amene anabalalitsa Israeli adzawasonkhanitsansondipo adzayangʼanira nkhosa zake ngati mʼbusa.’
11Pakuti Yehova wawombola fuko la Yakoboanawapulumutsa mʼdzanja la anthu owaposa mphamvu.
12Anthuwo adzabwera akuyimba mofuwula pa mapiri a Ziyoni;adzasangalala ndi zinthu zabwino zochokera kwa Yehova.Zinthu zabwinozo ndi izi: tirigu, vinyo watsopano ndi mafuta,ana ankhosa ndi ana angʼombe.Iwo adzakhala ngati munda wothiriridwa bwino,ndipo sadzamvanso chisoni.
13Pamenepo anamwali adzavina ndi kusangalala.Anyamata ndi okalamba nawonso adzasangalala.Kulira kwawo ndidzakusandutsa chisangalalo;ndidzawasangalatsa nʼkuchotsa chisoni chawo.
20Kodi Efereimu si mwana wanga wokondedwa,mwana amene Ine ndimakondwera naye?Ngakhale nthawi zambiri ndimamudzudzula,ndimamukumbukirabe.Kotero mtima wanga ukumufunabe;ndimamumvera chifundo chachikulu kwambiri,”akutero Yehova.
20
21“Muyike zizindikiro za mu msewu;muyimike zikwangwani.Yangʼanitsitsani msewuwo,njira imene mukuyendamo.Bwerera, iwe namwali wa Israeli,bwerera ku mizinda yako ija.
22Udzakhala jenkha mpaka liti,iwe mwana wa mkazi wosakhulupirika?Yehova walenga chinthu chatsopano pa dziko lapansi; mkazi ndiye tsopano aziteteza mwamuna.”
23Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti, “Ndikadzabwera nawo anthuwa kuchokera ku ukapolo, anthu a mʼdziko la Yuda ndi amene akukhala mʼmizinda yake adzayankhulanso mawu akuti, ‘Yehova akudalitse, iwe malo achilungamo, iwe phiri lopatulika.’
24Anthu adzakhala ku Yuda ndi ku mizinda yake pamodzi ndi alimi ndi oweta nkhosa.
35Yehova akuti, Iye amene amakhazikitsa dzuwakuti liziwala masana,amene amalamula kuti mwezi ndi nyenyeziziziwala usiku,amene amavundula nyanjakuti mafunde akokome,dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse:
36Ngati zimenezi zilekeka pamaso panga, akutero Yehova, pamenepo padzakhala pamathero a fuko la Israeli pamaso panga.
37Yehova akuti, “Ndidzataya fuko la Israeli chifukwa cha machimo awo.Ngati patapezeka munthuamene angathe kupima zakuthambonʼkufufuza maziko a dziko lapansi.”
38“Taonani masiku akubwera,” akutero Yehova, “pamene mzinda wa Yehova udzamangidwanso kuyambira ku Nsanja ya Hananeli mpaka ku Chipata cha Ngodya.
39Malire ake adzayambira pamenepo kupita ku phiri la Garebu, nʼkudzakhota kuloza ku Gowa.
40Chigwa chonse mʼmene amatayiramo mitembo ndi phulusa, ndiponso minda yonse kuyambira ku Chigwa cha Kidroni mpaka ku ngodya ya Chipata cha Akavalo mbali ya kummawa, adzakhala malo opatulika a Yehova. Mzindawu sadzawuzulanso kapena kuwuwononga.”