1“Ngati mukufuna kubwerera, inu Aisraeli,bwererani kwa Ine,”akutero Yehova.“Chotsani mafano anu onyansa pamaso pangandipo musasocherenso.
2Muzilumbira mokhulupirika ndiponso mwa chilungamokuti, ‘Pali Yehova wamoyo.’Mukatero anthu a mitundu ina yonse adzandipempha kuti ndiwadalitsendipo adzanditamanda.”
3Zimene Yehova akunena kwa anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu ndi izi: “Limani masala anumusadzale pakati pa minga.
4Dziperekeni nokha kwa Inekuti munditumikire ndi mtima wanu wonse,inu anthu a ku Yuda ndi ku Yerusalemu.Muzichita zimenezi kuopa kuti mkwiyo wanga ungabuke ngati moto ndi kukutenthani,chifukwa cha ntchito zanu zoyipazopopanda wina wowuzimitsa.
5“Lengeza ku Yuda ndi kulalikira mu Yerusalemu kuti,‘Lizani lipenga mʼdziko lonse!’Ndipo fuwulani kuti,‘Sonkhanani!Tiyeni tithawire ku mizinda yotetezedwa!’
6Kwezani mbendera kuyangʼana ku Ziyoni!Musachedwe, thawani kuti mupulumuke!Pakuti Ine ndikubweretsa chilango kuchokera kumpoto,kudzakhala chiwonongeko choopsa.”
6
7Monga mkango umatulukira mʼngaka yakemomwemonso wowononga mayikowanyamuka ndi kutuluka ku mbuto yake.Watero kuti awononge dziko lanu.Mizinda yanu idzakhala mabwinjapopanda wokhalamo.
8Choncho valani ziguduli,lirani ndi kubuwula,pakuti mkwiyo waukulu wa Yehovasunatichokere.
8
9“Pa tsiku limenelo, mfumu ndi nduna zake adzataya mtima,ansembe adzachita mantha kwambiri,ndipo aneneri adzathedwa nzeru,”akutero Yehova.
10Ndipo ine ndinati, “Haa, Ambuye Yehova, ndithu munawanyenga anthu awa pamodzi ndi Yerusalemu pamene munanena kuti, ‘Mudzakhala pa mtendere,’ chonsecho lupanga lili pakhosi pathu.”
11Nthawi imeneyo anthu awa ndi Yerusalemu adzawawuza kuti, “Mphepo yotentha yochokera ku magomo a mʼchipululu ikuwomba pa anthu anga, osati mphepo yopeta kapena yoyeretsa;
12koma mphepo yamphamvu kwambiri yochokera kwa Ine. Tsono ndi Ineyo amene ndikuwaweruza.”
14Iwe Yerusalemu, tsuka mtima wako kuchotsa zoyipa kuti upulumuke.Kodi maganizo ako oyipawo udzakhala nawo mpaka liti?
15Pakuti amithenga akulalika mawu mʼdziko la Dani;akulengeza za masautso kuchokera ku mapiri a Efereimu.
16Iwo akuti, “Fotokozani zimenezi kwa anthu a mitundu ina,lengezani zimenezi mu Yerusalemu kuti,‘Ankhondo akubwera kuchokera ku dziko lakutali,akufuwula ndi kudzazinga mizinda ya Yuda.
21Kodi ndikhale ndikuona mbendera ya nkhondo,ndi kumva kulira kwa lipenga mpaka liti?
21
22Yehova akuti, “Anthu anga ndi zitsiru;iwo sandidziwa.Iwo ndi ana opanda nzeru;samvetsa chilichonse.Ali ndi luso lochita zoyipa,koma sadziwa kuchita zabwino.”
29Pakumva phokoso la okwera pa akavalo ndi la anthu oponya mivi,anthu a mʼmizinda adzathawa.Ena adzabisala ku nkhalango;ena adzakwera mʼmatanthwemizinda yonse nʼkuyisiya;popanda munthu wokhalamo.
31Ndikumva kulira ngati kwa mayi pa nthawi yake yobereka,kubuwula ngati kwa mayi amene akubereka mwana wake woyamba.Kuliraku ndi kwa anthu a mu Ziyoni, wefuwefu.Atambalitsa manja awo nʼkumati,“Kalanga ife! Tikukomoka.Moyo wathu waperekedwa kwa anthu otipha.”