2Yehova akuti, “Taonani mmene madzi akubwerera kuchokera kumpoto; adzasanduka mtsinje wosefukira ndi a mkokomo. Adzasefukira mʼdziko monse ndi kumiza chilichonse mʼmenemo, mizinda ndi onse okhala mʼmenemo. Anthu adzafuwula; anthu onse okhala mʼdzikomo adzalira
3akadzamva mgugu wa ngʼombe zazimuna zothamanga, phokoso la magaleta ake ndi kulira kwa mikombero yake. Makolo sadzatembenuka kuti athandize ana awo; manja awo adzangoti khoba.
4Pakuti tsiku lafika lowononga Afilisti onse ndi kupha onse otsala, onse amene akanatha kuthandiza Turo ndi Sidoni. Yehova ali pafupi kuwononga Afilisti, otsala ochokera ku zilumba za ku Kafitori.
5Anthu a ku Gaza ameta mipala; anthu a ku Asikeloni akhala chete. Inu otsala a ku chigwa, mudzakhala mukudzichekacheka mpaka liti?