1Yehova ananena izi: Amoni, “Kodi Israeli alibe ana aamuna?Kapena alibe mlowamʼmalo?Tsono nʼchifukwa chiyani anthu opembedza Moleki alanda dziko la Gadi?Nʼchifukwa chiyani anthu ake akukhala mʼmizinda ya Gadi?
2Koma nthawi ikubwera,”akutero Yehova,“pamene ndidzamveketse mfuwu wankhondoku Raba, likulu la Amoni;ndipo malo awo opembedzera milungu yawoadzatenthedwa ndi moto.Choncho Aisraeli adzalandanso dziko lawokuchokera kwa amene anawalanda poyamba dzikolo,”akutero Yehova.
3“Lirani, inu anthu a ku Hesiboni chifukwa wowononga uja wafika!Fuwulani, inu anthu okhala ku Raba!Valani ziguduli ndi kulira mwamphamvu;thamangani uku ndi uku mʼkati mwa malinga,chifukwa mulungu wanu Moleki adzapita ku ukapolo,pamodzi ndi ansembe ake ndiponso akuluakulu ake.
7Yehova Wamphamvuzonse ananena izi za Edomu: “Kodi nzeru sizikupezekanso ku Temani?Kodi anzeru analeka kupereka uphungu?Kodi nzeru zawo zinatheratu?
8Inu anthu a ku Dedani, thawani,bwererani ndi kukabisala ku makwalalachifukwa ndidzagwetsa mavuto pa zidzukulu za Esaupopeza nthawi yawo ya chiweruzo yafika.
13Ine ndikulumbira, akutero Yehova, kuti mzinda wa Bozira udzasanduka bwinja, chinthu chochititsa mantha, chomachiseka ndiponso chotembereredwa. Mizinda yake yonse idzakhala mabwinja mpaka muyaya.”
14Ndamva uthenga wochokera kwa Yehova:Nthumwi yatumidwa kupita kwa anthu a mitundu ina kukanena kuti,“Sonkhanani pamodzi kuti muthire nkhondo Edomu!Konzekerani nkhondo!”
15“Ndidzakuchepetsani pakati pa anthu a mitundu ina.Mudzakhala anthu onyozeka pakati pa anthu.
17“Dziko la Edomu lidzasanduka chinthu chochititsa mantha.Onse odutsamo adzadabwa ndi kupukusa mitu yawochifukwa cha kuwonongeka kwake.
18Monga momwe anawonongekera Sodomu ndi Gomora,pamodzi ndi mizinda yake yozungulira,”akutero Yehova,“motero palibe munthuamene adzakhala mu Edomu.
18
19“Monga mkango wotuluka ku nkhalango za ku Yorodanikupita ku malo a msipu wobiriwira,Ine ndidzapirikitsa anthu a ku Edomu mwadzidzidzi kuchoka mʼdziko lawo.Pambuyo pake ndidzawayikira owalamulira amene ndamufuna Ine.Kodi ndani wofanana nane, ndipo angatsutsane nane ndani?Ndipo ndi mʼbusa uti amene angalimbane nane?”
20Nʼchifukwa chake imvani. Izi ndi zimene Ine Yehovandakonza zolangira anthu a ku Edomu ndi a ku Temani.Ngakhale ana omwe adzatengedwa ukapolondipo aliyense adzachita mantha chifukwa cha iwo.
21Akadzagwa Edomu padzakhala mfuwu waukulu ndipo dziko lapansi lidzanjenjemera;kulira kwawo kudzamveka mpaka ku Nyanja Yofiira.
22Taonani, mtundu wina udzachita kuwulukanʼkudzatera pa Bozira ngati chiwombankhanga chimene chatambalitsa mapiko ake.Pa tsiku limenelo mitima ya ankhondo a ku Edomuidzagunda ngati mtima wa mayi pa nthawi yake yochira.
23Mawu a Yehova onena za Damasiko ndi awa: “Anthu a ku Hamati ndi a ku Aripadi akuchita manthachifukwa amva nkhani yoyipa.Mitima yawo yagwidwa ndi manthandipo ali ngati muja ichitira nyanja yosakhazikika.
24Anthu a ku Damasiko alefuka.Abwerera mʼmbuyo kufuna kuthawachifukwa agwidwa ndi mantha aakulu.Ali ndi nkhawa komanso manthangati za mayi pa nthawi yake yochira.
26Nʼchifukwa chake anyamata ake adzagwa mʼmisewu ndi kufa;ankhondo ake onse adzawonongedwa tsiku limenelo,”akutero Yehova Wamphamvuzonse.
27“Ndidzatentha malinga a Damasiko;moto udzanyeketsa nyumba zaufumu za Beni-Hadadi.”
28Mawu a Yehova onena za Kedara ndi maufumu a ku Hazori, amene Nebukadinezara mfumu ya Babuloni anawagonjetsa ndi awa: “Nyamukani mukathire nkhondo ku Kedara.Kawonongeni anthu a kummawako.
29Landani matenti awo ndi nkhosa zawo,ndiye kuti, mutenge nsalu zawo ndi katundu wawo.Mutengenso ngamira zawo.Anthu adzafuwula kwa iwo kuti,‘Kuli zoopsa mbali zonse!’
29
30“Thawani mofulumira!Kabisaleni mʼmakhwawa, inu anthu ku Hazori,”akutero Yehova.“Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni wakukonzerani chiwembu;wakonzekera zoti alimbane nanu.
30
31“Nyamukani kathireni nkhondo mtundu wa anthu umene uli pamtendere,umene ukukhala mosatekeseka,”akutero Yehova,“mzindawo ulibe zipata ngakhalenso mipiringidzo;anthu ake amakhala pa okha.
32Ngamira zawo zidzafunkhidwa,ndipo makola a ngʼombe zawo adzalandidwa.Ndidzabalalitsira ku mphepo zinayi onse amene amameta tsitsi lawo chamʼmbali.Ndidzawagwetsera mavuto kuchokera ku mbali zonse,”akutero Yehova.
36Ndidzabweretsa mphepo zinayi pa Elamukuchokera ku zigawo zinayi zamlengalenga;ndidzawabalalitsira ku mphepo zinayi,ndipo sipadzakhala dzikolimene anthu a ku Elamu sadzafikako.
37A ku Elamuwo ndidzachititsa mantha pamaso pa adani awokomanso pamaso pa iwo amene akufuna kuwononga moyo wawo.Ndidzawagwetsera mkwiyo wangandipo adzakhala pa mavuto,”akutero Yehova.“Ndidzawapirikitsa ndi lupangampaka nditawatheratu.
38Ndidzakhazika mpando wanga waufumu ku Elamundipo ndidzawononga mfumu yake pamodzi ndi akuluakulu ake,”akutero Yehova.
38
39“Komabe mʼtsogolomo ndidzabwezeraanthu a ku Elamu dziko lawo,”akutero Yehova.