3Inu Yehova, kodi suja mumafuna anthu onena zoona?Inu munawakantha anthuwo, koma sanamve kupweteka;munawaphwanya anthuwo, koma sanatengepo phunziro.Anawumitsa mitima yawo ngati mwalandipo anakaniratu kulapa.
4Ndiye ndinati, “Awa ndi amphawi chabe;anthu ochita zopusa.Sadziwa njira ya Yehova,sazindikira zimene Mulungu wawo amafuna.
5Tsono ndidzapita kwa atsogolerindi kukayankhula nawo;ndithu iwo amadziwa njira ya Yehova,amadziwa zomwe Mulungu wawo amafuna.”Koma ayi, iwonso anathyola goli la Yehovandipo anadula msinga zawo.
6Choncho mkango wochokera ku nkhalango udzawapha,mmbulu wochokera ku thengo udzawawononga,kambuku adzawabisalira pafupi ndi mizinda yawokuti akhadzule aliyense amene adzayesera kutuluka mʼmizindamopakuti kuwukira kwawo ndi kwakukulundipo abwerera mʼmbuyo kwambiri.
6
7Yehova akuti, “Kodi ndingakukhululukireni bwanji ndi zimene mwachita?Ana anu andisiya Inendipo amapembedza milungu imene si milungu konse.Ine ndinawapatsa zonse zimene ankasowa,komabe iwo anachita chigololonamasonkhana ku nyumba za akazi achiwerewere.
8Monga amachitira akavalo onenepa akamamemesa,aliyense wa iwo ankathamangira mkazi wa mnzake.
9Tsono ndingaleke kuwalanga chifukwa cha zimenezi?”akutero Yehova.“Kodi nʼkuleka kuwulipsiramtundu woterewu?
9
10“Pitani ku minda yake ya mipesa ndi kukayiwononga,koma musakayiwononge kotheratu.Sadzani nthambi zakepakuti anthu amenewa si a Yehova.
11Nyumba ya Israeli ndi nyumba ya Yudaonse akhala osakhulupirika kotheratu kwa Ine.”
16Zida zawo za nkhondo zapha anthu ambirimbiri;onsewo ndi ankhondo amphamvu okhaokha.
17Adzakudyerani zokolola zanu ndi chakudya chanu,adzapha ana anu aamuna ndi aakazi;adzakupherani nkhosa zanu ndi ngʼombe zanu,adzawononga mpesa wanu ndi mikuyu yanu.Ndi malupanga awo adzagwetsamizinda yanu yotetezedwa imene mumayidalira.
18“Komabe pa masiku amenewo sindidzakuwonongani kotheratu,” akutero Yehova.
19Ndipo pamene anthu adzafunsa Yehova kuti, “Chifukwa chiyani Yehova Mulungu wathu wachita zimenezi?” Iwe udzawawuze kuti, “Monga momwe mwasiyira Ine ndi kutumikira milungu yachilendo mʼdziko mwanu, momwemonso mudzatumikira anthu a mʼdzikonso lachilendo.”
20“Lengeza izi kwa ana a Yakobondipo mulalikire kwa anthu a ku Yuda kuti,
21Imvani izi, inu anthu opusa ndi opanda nzeru,inu amene maso muli nawo koma simupenya,amene makutu muli nawo koma simumva.
22Kodi simuyenera kuchita nane mantha?”Akutero Yehova.“Kodi simuyenera kunjenjemera pamaso panga?Ine ndinayika mchenga kuti ukhale malire a nyanja,malire a muyaya amene nyanjayo singadutsepo.Mafunde angawombe motani, koma sangathe kupitirira malirewo;mafunde angakokome motani, koma sangadutse malirewo.
23Koma anthu awa ndi nkhutukumve ndiponso a mitima yowukira;andifulatira ndipo andisiyiratu.
24Sananenepo mʼmitima mwawo kuti,‘Tiyeni tizipembedza Yehova Mulungu wathu.Kodi suja amatipatsa pa nthawi yake mvula yachizimalupsa ndi yamasika.Iye salephera konse kutipatsa nyengo ya kholola.’
25Koma zolakwa zanu zalepheretsa zonsezi;ndipo machimo anu akumanitsani zabwino.
27Nyumba zawo zadzaza ndi chuma chochipeza mwa chinyengongati zikwere zodzaza ndi mbalame.Nʼchifukwa chake asanduka otchuka ndi olemera.
28Ndipo ananenepa ndi kukhala ndi matupi osalala.Ntchito zawo zoyipa nʼzopanda malire;saweruza mwachilungamo nkhani ya ana amasiye kuti iyende bwino,sateteza ufulu wa anthu osauka.
29Kodi Ine ndingaleke kuwalanga chifukwa cha zimenezi?Kodi ndisawulipsiremtundu woterewu?Akutero Yehova.
29
30“Chinthu chothetsa nzeru ndi choopsa kwambirichachitika mʼdzikomo: