4Adzavulazidwa ndi kufera mʼdziko la Babulonilomwelo ndi mʼmisewu yawo yomwe.
5Pakuti Yuda ndi Israeli sanasiyidwe ngati amasiyendi Mulungu wawo, Yehova Wamphamvuzonse,koma ngakhale dziko la Babuloni ndi lodzaza ndi machimopamaso pa Woyerayo wa Israeli.
5
6“Thawaniko ku Babuloni!Aliyense apulumutse moyo wake!Musawonongeke naye pamodzi chifukwa cha machimo ake.Imeneyi ndi nthawi yoti Yehova amulange;Yehova adzamulipsira.
7Babuloni anali ngati chikho cha golide mʼdzanja la Yehova;kuti aledzeretse dziko lonse lapansi.Mitundu yambiri ya anthu inamwa vinyo wake;nʼchifukwa chake tsopano inachita misala.
8Babuloni wagwa mwadzidzidzi ndi kusweka.Mulireni!Mfunireni mankhwala opha ululu wake;mwina iye nʼkuchira.”
8
9Ena anati, “ ‘Ife tinayesa kumupatsa mankhwala Babuloni,koma sanachire;tiyeni timusiye ndipo aliyense apite ku dziko la kwawo,pakuti mlandu wake wafika mpaka mlengalenga,wafika mpaka kumwamba.’
11“Yehova wadzutsa mitima ya mafumu a Amedi,popeza cholinga chake ndi kuwononga Babuloni.Motero adzalipsira Ababulonichifukwa chowononga Nyumba yake.Ndiye Yehova akuti,‘Nolani mivi, tengani zishango.’
12Kwezani mbendera yankhondo kuti muwononge malinga a Babuloni!Limbitsani oteteza,ikani alonda pa malo awo,konzekerani kulalira.Pakuti Yehova watsimikizandipo adzachitadi zomwe ananena za anthu a ku Babuloni.
15“Yehova analenga dziko lapansi ndi mphamvu zake;Iye anapanga dziko lonse ndi nzeru zakendipo anayala thambo mwaluso lake.
16Iye akayankhula, kumamveka mkokomo wamadzi akumwamba.Iyeyo amabweretsa mitambo kuchokera ku malekezero a dziko lapansi.Amabweretsa mphenzi pamodzi ndi mvulandi kutulutsa mphepo yamkuntho kumalo kumene amasungira.
16
17“Anthu onse ndi opusa ndiponso opanda nzeru;mmisiri aliyense wosula golide akuchita manyazi ndi mafano ake.Mafano akewo ndi abodza;alibe moyo mʼkati mwawo.
18Mafanowo ndi achabechabe, zinthu zosekedwa nazo.Pamene anthuwo azidzaweruzidwa mafanowo adzawonongedwa.
19Koma Yehova amene ndi Cholowa cha Yakobo sali ngati mafanowo.Iyeyu ndi Mlengi wa zinthu zonse,kuphatikizapo mtundu umene anawusankha kuti ukhale anthu ake.Dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse.
19
20“Iwe Babuloni ndi ndodo yanga,chida changa chankhondo.Ndi iwe ndimaphwanya mitundu ya anthu,ndi iwe ndimawononga maufumu,
21ndi iwe ndimaphwanya kavalo ndi wokwerapo,ndi iwe ndimaphwanya galeta ndi woyendetsa wake.
22Ndi iwe ndimaphwanya mwamuna ndi mkazi,ndi iwe ndimaphwanya nkhalamba ndi wachinyamata,ndi iwe ndimaphwanya mnyamata ndi namwali.
23Ndi iwe ndimaphwanya mʼbusa ndi ziweto,ndi iwe ndimaphwanya mlimi ndi ngʼombe,ndi iwe ndimaphwanya abwanamkubwa ndi atsogoleri a ankhondo.
24“Inu mukuona ndidzalanga Babuloni ndi onse amene amakhala mʼdziko la Babuloni chifukwa cha zolakwa zonse anachita ku Ziyoni,” akutero Yehova.
33Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti, “Babuloni wokongola uja wakhala ngati malo opunthirapo tirigupa nthawi yake yopuntha tirigu; A ku Yerusalemu akuti,Posachedwapa nthawi yake yomukolola ifika.”
34A ku Yerusalemu akuti, “Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni watiwononga,watiphwanya,ndi kutitaya ngati mbiya yopanda kanthu.Watimeza ngati ngʼona,wakhuta ndi zakudya zathu zokoma,kenaka nʼkutilavula.”
35Anthu a ku Ziyoni anene kuti,“Zankhanza zimene anatichitira ife ziwabwerere Ababuloni.”Anthu okhala mu Yerusalemu anene kuti,“Magazi athu amene anakhetsedwa akhale pa amene akukhala ku Babuloni.”
47Pakuti taonani, nthawi ikubwera ndithupamene ndidzalanga mafano a ku Babuloni;dziko lake lonse lidzachita manyazindi ophedwa ake onse adzakhala ngundangunda pakati pake.
48Pamenepo kumwamba ndi dziko lapansi ndi zonse zili mʼmenemozidzayimba mokondwa chifukwa cha kugwa kwa Babuloni.Anthu owononga ochokera kumpotoadzamuthira nkhondo,”akutero Yehova.
48
49“Babuloni anapha anthu ambiri pa dziko lapansi.Tsono, nawo anthu a ku Babuloni ayenera kuphedwachifukwa anapha anthu a ku Yerusalemu.
50Inu amene munapulumuka ku nkhondo ya Babuloni,chokani pano ndipo musazengereze!Kumbukirani Yehova ngakhale muli ku mayiko akutali,ganizirani za Yerusalemu.”
50
51Inu mukuti, “Tikuchita manyazi,chifukwa tanyozedwandipo nkhope zathu zili ndi manyazi,chifukwa anthu achilendo alowamalo opatulika a Nyumba ya Yehova.”
51
52Nʼchifukwa chake Yehova akuti,“Masiku akubwera pamene ndidzalanga mafano ake,ndipo mʼdziko lake lonseanthu ovulala adzabuwula.
54“Imvani mfuwu wolira kuchokera ku Babuloni.Imvani phokoso lachiwonongeko chachikulukuchokera mʼdziko la Babuloni.
55Pakuti Yehova akuwononga Babuloni,ndipo akuthetsa phokoso lake lalikulu.Mfuwu wa adani ukumveka ngati mkokomo wa madzi ambiri.Phokoso lawo likunka likwererakwerera.
56Pakuti wowononga wafika kudzamenyana ndi Babuloni,ankhondo ake agwidwa,ndipo mauta awo athyoka.Paja Yehova ndi Mulungu wobwezera chilango;adzabwezera kwathunthu.
57Ndidzaledzeretsa akuluakulu ake pamodzi ndi anzeru ake,abwanamkubwa ake, atsogoleri a ankhondo pamodzinso ndi ankhondo;adzagona kwamuyaya osadzukanso,”akutero Mfumu, amene dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse.
58Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Malinga aakulu a Babuloni adzasalazidwandipo zipata zake zazitali zidzatenthedwa;mitundu ya anthu inangogwira ntchito pachabe.Anthu anatopa ndi kumanga zimene tsopano zikupsa ndi moto.”
59Zedekiya mfumu ya Yuda inali ndi phungu wake wamkulu amene dzina lake linali Seraya mwana wa Neriya chidzukulu cha Maseya. Mʼchaka chachinayi cha ulamuliro wake, Zedekiya anapita ndi Seraya ku Babuloni. Tsono mneneri Yeremiya anamupatsirako uthenga Serayayo.
60Yeremiya anali atalemba mʼbuku za masautso onse amene adzafike pa Babuloni ndi zina zonse zokhudza Babuloni.