1“Thawani, inu anthu a ku Benjamini!Tulukani mu Yerusalemu!Lizani lipenga ku Tekowa!Kwezani mbendera ku Beti-Hakeremu!Pakuti tsoka lalikulu likubwera kuchokera kumpoto,ndipo chiwonongekocho nʼchachikulu.
2Kodi mzinda wa Ziyoni suli ngati msipu wokongola kwambiri,kumene abusa amafikako ndi ziweto zawo?
6Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Dulani mitengondipo mumange mitumbira yankhondo kulimbana ndi Yerusalemu.Mzinda umenewu uyenera kulangidwa;wadzaza ndi kuponderezana.
7Monga momwe chitsime chimatulutsira madzindi mmenenso Yerusalemu amatulutsira zoyipa zake.Chiwawa ndi chiwonongeko ndi zomwe zimamveka mu mzindamo;nthenda yake ndi mabala ake ndimaziona nthawi zonse.
8Iwe Yerusalemu, tengapo phunziro,kuopa kuti chikondi changa pa iwe chingakuchokerendi kusandutsa dziko lako kukhala bwinjamopanda munthu wokhalamo.”
10Kodi ndiyankhule ndi yani ndi kumuchenjeza?Ndinene mawu ochenjeza kwa yani kuti amve?Makutu awo ndi otsekekakotero kuti sangathe kumva.Mawu a Yehova ndi onyansa kwa iwo;sasangalatsidwa nawo.
11Koma ine ndadzazidwa ndi mkwiyo wa Yehova,ndipo ndatopa ndi kusunga mkwiyo wa Yehova.
11Yehova anandiwuza kuti, “Tsono ndidzawutulutsira mkwiyo umenewu pa ana oyenda mʼmisewu ndi pa achinyamata amene asonkhana pamodzi;pakutinso mwamuna ndi mkazi wake adzatengedwa,pamodzi ndi okalamba amene ali ndi zaka zochuluka.
12Nyumba zawo adzazipereka kwa ena,pamodzi ndi minda yawo ndi akazi awo.Ndidzatambasula dzanja langa kukanthaanthu okhala mʼdzikomo,”akutero Yehova.
13“Kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu,onse ali ndi dyera lofuna kupeza phindu mwa kuba;aneneri pamodzi ndi ansembe omwe,onse amachita zachinyengo.
18Nʼchifukwa chake imvani, inu anthu a mitundu ina;yangʼanitsitsani, inu amene mwasonkhana pano,chimene chidzawachitikire anthuwo.
19Imvani, inu anthu okhala pa dziko lapansi,ndikubweretsa masautso pa anthu awa.Zimenezi ndi mphotho ya ntchito zawo.Iwowa sanamvere mawu angandipo anakana lamulo langa.
20Kodi pali phindu lanji ngakhale mubwere ndi lubani kuchokera ku Seba,kapena zonunkhira zina kuchokera ku dziko lakutali?Nsembe zanu zopsereza Ine sindidzalandira;nsembe zanu sizindikondweretsa.”
21Choncho Yehova akuti, “Ndidzayika zokhumudwitsa pamaso pa anthu awa.Abambo ndi ana awo aamuna onse adzapunthwa ndi kugwa;anansi awo ndi abwenzi awo adzawonongeka.”
22Yehova akunena kuti, “Taonani, gulu lankhondo likubwerakuchokera kumpoto;mtundu wa anthu amphamvu wanyamukakuchokera kumathero a dziko lapansi.
23Atenga mauta ndi mikondo;ndi anthu ankhanza ndi opanda chifundo.Phokoso lawo lili ngati mkokomo wa nyanja.Akwera pa akavalo awondipo akonzekera ngati anthu ankhondo,kudzakuthirani nkhondo anthu a ku Ziyoni.”
23
24A ku Ziyoni akuti “Ife tamva mbiri yawo,ndipo manja anthu alefukiratu.Nkhawa yatigwira,ndipo tikumva ululu ngati mayi pa nthawi yake yochira.
25Musapite ku mindakapena kuyenda mʼmisewu,pakuti mdani ali ndi lupanga,ndipo ponseponse anthu akuchita mantha.
26Inu anthu anga, valani zigudulindipo gubudukani pa phulusa;lirani mwamphamvungati munthu wolirira mwana wake mmodzi yekha,pakuti mwadzidzidzi wowonongayoadzabwera kudzatipha.
28Onsewo ali ndi khalidwe lokanika ndi lowukirandipo akunka nanena zamiseche.Iwo ndi olimba ngati mkuwa ndi chitsulo.Onse amangochita zoyipa zokhazokha.
29Moto mu mvukuto ukuyaka kwambiri;mtovu watha kusungunuka ndi moto.Koma ntchito yosungunulayo sikupindulachifukwa zoyipa sizikuchokapo.
30Iwo ali ngati siliva wotayidwa,chifukwa Yehova wawakana.”