4“Aliyense achenjere ndi abwenzi ake;asadalire ngakhale abale ake.Aliyense amafuna kumudyera mʼbale wake masuku pa mutu.Choncho aliyense amachitira bwenzi lake ugogodi.
7Nʼchifukwa chake Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Taonani, Ine ndidzawasungunula ngati chitsulo ndi kuwayesa.Kodi ndingachite nawonsobwanji chifukwa cha machimo awo?
8Lilime lawo lili ngati muvi wakuthwa;limayankhula zachinyengo.Aliyense ndi pakamwa pake amayankhula mawu achikondi kwa mnansi wake,koma mu mtima mwake amakonzekera zomuchita chiwembu.
9Kodi ndilekerenji kuwalanga chifukwa cha zimenezi?akutero Yehova.‘Kodi ndisawulipsiremtundu wotere wa anthu?’ ”
9
10Ndidzakhetsa misozi ndi kulira kwamphamvu chifukwa cha mapirindipo ndidzadandaula chifukwa cha msipu wa ku chipululu.Malo onsewo awonongeka ndipo palibe amene amapitako,ndipo sikumveka kulira kwa ngʼombe.Mbalame zamlengalenga zathawandipo nyama zakuthengo zachokako.
15Tsono chimene Ine Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli ndidzachite ndi anthu amenewa ndi ichi: “Ndidzawadyetsa chakudya cha ziphe ndi kuwamwetsa madzi a ndulu.
16Ndidzawabalalitsa pakati pa mitundu ya anthu imene iwowo kapena makolo awo sanayidziwe, ndipo ndidzawalondola ndi ankhondo mpaka nditawawononga.”
20Tsono inu amayi, imvani mawu a Yehova;tcherani makutu anu kuti mumve mawu a Yehova.Phunzitsani ana anu aakazi kulira mwachisoni;aliyense aphunzitse mnzake nyimbo ya maliro.
24koma ngati munthu akufuna kunyadira, anyadire chinthu ichi:kuti iye amamvetsa za Ine ndipo amandidziwa,kuti ndine Yehova, amene ndimakonda chifundo,chilungamo ndiponso ungwiro pa dziko lapansi.Zimenezi ndizo ndimakondwera nazo,”akutero Yehova.
25“Nthawi ikubwera,” akutero Yehova, “pamene ndidzalanga onse amene anachita mdulidwe koma mu mtima sasamala nʼkomwe.
26Ndidzalanga anthu a ku Igupto, Yuda, Edomu, Amoni, Mowabu, ndiponso onse amene amakhala kutali ku chipululu. Mitundu ina yonseyi ndi yosachita mdulidwe, ngakhalenso Aisraeli nawonso sanachite mdulidwe wa mu mtima.”