1Masomphenya wonena za Yuda ndi Yerusalemu, amene Yesaya mwana wa Amozi, anaona pa nthawi ya ulamuliro wa Uziya, Yotamu, Ahazi ndi Hezekiya, mafumu a Yuda.
2Tamverani, miyamba inu! Tchera khutu, iwe dziko lapansi!Pakuti Yehova wanena kuti,“Ndinabala ana ndi kuwalera,koma anawo andiwukira Ine.
4Haa, mtundu wochimwa,anthu olemedwa ndi machimo,obadwa kwa anthu ochita zoyipa,ana odzipereka ku zoyipa!Iwo asiya Yehova;anyoza Woyerayo wa Israelindipo afulatira Iyeyo.
6Kuchokera ku phazi mpaka ku mutupalibe pabwino,paliponse pali mikwingwirima ndi zilonda,mabala ali magazi chuchuchu,mabala ake ngosatsuka, ngosamangandiponso ngosapaka mafuta ofewetsa.
6
7Dziko lanu lasanduka bwinja,mizinda yanu yatenthedwa ndi moto;minda yanu ikukololedwa ndi alendoinu muli pomwepo,dziko lanu lasanduka bwinja monga ngati lagonjetsedwa ndi alendo.
8Mwana wamkazi wa Ziyoni watsala yekhangati nsanja mʼmunda wampesa,ngati chisimba mʼmunda wa minkhaka,ngati mzinda wozingidwa ndi nkhondo.
9Yehova Wamphamvuzonse akanapandakutisiyira opulumuka,tikanawonongeka ngati Sodomu,tikanakhala ngati anthu a ku Gomora.
9
10Imvani mawu a Yehova,inu olamulira Sodomu;mverani lamulo la Mulungu wathu,inu anthu a ku Gomora!
11Yehova akuti, “Kodi ndili nazo chiyaninsembe zanu zochuluka?”“Zandikola nsembe zanu zopserezaza nkhosa zazimuna ndiponso mafuta a nyama zonenepa;sindikusangalatsidwansondi magazi angʼombe zamphongo ndi a ana ankhosa ndi ambuzi zazimuna.
12Ndani anakulamulirani kutimubwere nazo pamaso panga?Ndani anakuwuzani kuti muzipondaponda mʼmabwalo a nyumba yanga?
13Siyani kubweretsa nsembe zachabechabezo!Nsembe zanu zofukiza zimandinyansa Ine.Sindingapirire misonkhano yanu yoyipa,kapenanso zikondwerero za Mwezi Watsopano ndi Masabata.
14Zikondwerero zanu za Mwezi Watsopano ndi masiku anu opatulikandimadana nazo.Zasanduka katundu wondilemera;ndatopa kuzinyamula.
15Mukamatambasula manja anu popemphera,Ine sindidzakuyangʼanani;ngakhale muchulukitse mapemphero anu,sindidzakumverani.Manja anu ndi odzaza ndi magazi;
17phunzirani kuchita zabwino!Funafunani chilungamo,thandizani oponderezedwa.Tetezani ana amasiye,muwayimirire akazi amasiye pa milandu yawo.”
17
18Yehova akuti,“Tiyeni tsono tikambe mlandu wanu.Ngakhale machimo anu ali ofiira,adzayera ngati thonje.Ngakhale ali ofiira ngati kapezi,adzayera ngati ubweya wankhosa.
19Ngati muli okonzeka kundimveramudzadya zinthu zabwino za mʼdziko;
20koma mukakana ndi kuwukiramudzaphedwa ndi lupanga.”Pakuti Yehova wayankhula.
20
21Taonani momwe mzinda wokhulupirikawasandukira wadama!Mzinda umene kale unali wodzaza ndi chiweruzo cholungama;mu mzindamo munali chilungamo,koma tsopano muli anthu opha anzawo!
22Siliva wako wasanduka wachabechabe,vinyo wako wabwino wasungunulidwa ndi madzi.
23Atsogoleri ako ndi owukira,anthu ogwirizana ndi mbala;onse amakonda ziphuphundipo amathamangira mphatso.Iwo sateteza ana amasiye;ndipo samvera madandawulo a akazi amasiye.
24Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova Wamphamvu,Wamphamvuyo wa Israeli, akunena kuti,“Haa, odana nane ndidzawatha,ndipo ndidzawabwezera ndekha adani anga.
25Ndidzatambasula dzanja langa kuti ndilimbane nawe;ndidzasungunula machimo ako nʼkuwachotsa,monga mmene amachotsera dzimbiri ndi mankhwala.
26Ndidzabwezeretsa oweruza ako ngati masiku amakedzana,aphungu ako ndidzawabwezeretsa ngati poyamba paja.Kenaka iweyo udzatchedwamzinda wolungama,mzinda wokhulupirika.”
26
27Ziyoni adzawomboledwa mwa chiweruzo cholungama,anthu ake olapadi adzapulumutsidwa mwachilungamo.
28Koma owukira ndi ochimwa adzawawonongera pamodzi,ndipo amene asiya Yehova adzatheratu.
28
29“Mudzachita nayo manyazi mitengo ya thunduimene inkakusangalatsani;mudzagwetsa nkhope chifukwa cha mindaimene munayipatula.