2kuwalanda anthu osauka ufulu wawondi kumana chilungamo osautsidwa pakati pa anthu anga,amalanda zinthu za akazi amasiyendi kubera ana amasiye.
3Kodi mudzatani pa tsiku la chilango,pofika chiwonongeko chochokera kutali?Kodi mudzathawira kwa yani kuti akuthandizeni?Nanga chuma chanu mudzachisiya kuti?
4Kudzatsala nʼkungozolika mwamanyazi pakati pa anthu ogwidwakapena kufa pamodzi ndi ophedwa.Komabe pa zonsezi mkwiyo wake sunawachokere,mkono wake uli chitambasulire.
5“Tsoka kwa mfumu ya ku Asiriya, chikwapu cha mkwiyo wanga,iye ndiye ndodo ya mkwiyo wanga!
6Ndidzamutuma kukalimbana ndi mtundu wosapembedza Mulungu,ndidzamutumiza kukalimbana ndi anthu amene amandikwiyitsa Ine,kukafunkha ndi kulanda chuma,ndi kuwapondereza pansi ngati matope a mʼmisewu.
7Koma izi si zimene akufuna kukachita,izi si zimene zili mʼmaganizo mwake;cholinga chake ndi kukawononga,kukapulula mitundu yambiri ya anthu.
8Iye akuti, ‘Kodi atsogoleri anga ankhondo si mafumu okhaokha?’
16Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova Wamphamvuzonseadzatumiza matenda owondetsa kwa ankhondo amphamvu;kunyada kwa mfumuyo kudzapsandi moto wosazima.
17Mulungu, Kuwala kwa Israeli, adzakhala ngati moto,Woyera uja wa Israeli adzakhala ngati malawi a moto.Motowo udzawatentha ndi kuwapserezangati minga ndi mkandankhuku pa tsiku limodzi.
24Nʼchifukwa chake, Ambuye Yehova Wamphamvuzonse akunena kuti, “Inu anthu anga okhala mu Ziyoni,musawaope Asiriya,amene amakukanthani ndi ndodonakumenyani ndi zibonga monga mmene Igupto anachitira.
25Patsala pangʼonongʼono kuti mkwiyo wanga uchoke pa inundipo ndidzaonetsa ukali wanga pa iwo mpaka kuwawononga.”
25
26Yehova Wamphamvuzonse adzawakwapula ndi chikwapu,monga momwe anakwapulira Amidiyani ku thanthwe la Orebu;ndipo adzatukula ndodo yake pa madzindikuwalanga monga analangira Igupto pa nyanja.
27Tsiku limenelo katundu wawo adzachotsedwa pa mapewa anu,goli lawo lidzachoka mʼkhosi mwanu;golilo lidzathyokachifukwa cha kunenepa kwambiri.
27
28Adani alowa mu Ayatiapyola ku Migironi;asunga katundu wawo ku Mikimasi.
29Adutsa pa mpata uja, ndipo akuti,“Tikagona ku Geba”Rama akunjenjemera;Gibeya, mzinda wa Saulo ukuthawa.
30Lilani mokweza, inu anthu a ku Galimu!Tchera khutu, iwe Laisa!Iwe Anatoti wosauka!
31Anthu a ku Madimena akuthawa;anthu a ku Gebimu bisalani.
32Lero lomwe lino adaniwo adzayima ku Nobu;adzagwedeza mikono yawo,kuopseza anthu a ku Ziyoni,pa phiri la Yerusalemu.