8Mwana wakhanda adzasewera pa dzenje la mamba,ndipo mwana wamngʼono adzapisa dzanja lake ku phanga la mphiri osalumidwa.
9Sipadzakhala chilichonse chopweteka kapena chowonongapa phiri lopatulika la Yehova,pakuti anthu a dziko lapansi adzadzaza ndi nzeru yotha kudziwa Yehovamonga momwe nyanja imadzazira ndi madzi.
10Tsiku limenelo mfumu yatsopano yochokera pa Muzu wa Yese idzakhala ngati chizindikiro kwa anthu a mitundu yonse. Mitundu ya anthu idzasonkhana kwa Iye, ndipo malo awo okhalapo adzakhala aulemerero.
11Tsiku limenelo Ambuye adzatambasula dzanja lake kachiwiri kuti awombole anthu ake otsalira ku Asiriya, ku Igupto, ku Patirosi, Kusi, ku Elamu, ku Sinana, ku Hamati ndi pa zilumba za nyanja yamchere.
12Adzakwezera mitundu ya anthu mbendera,ndipo adzasonkhanitsa otayika a ku Israeli;Iye adzasonkhanitsa anthu obalalika a ku Yudakuchokera ku mbali zonse zinayi za dziko lapansi.
13Nsanje ya Efereimu idzatha,ndipo adani a Yuda adzatha;Efereimu sadzachitira nsanje Yuda,ngakhale Yuda sadzamuda Efereimu.
14Yuda ndi Efereimu adzathira nkhondo pa Afilisti mbali ya kumadzulo;ndipo onsewo pamodzi adzalanda zinthu za anthu a kummawa.Adzalimbana ndi Edomu ndi Mowabu,ndipo Aamoni adzawagonjera.
15Yehova adzaphwetsamwendo wa nyanja ya Igupto;adzatambasula dzanja lake ndipo adzawombetsa mphepo yotenthapa mtsinje wa Yufurate.Iye adzawugawa mtsinjewo kukhala timitsinje tisanu ndi tiwirikuti anthu athe kuwoloka powuma atavala nsapato.
16Padzakhala msewu waukulu woti ayendepo anthu ake otsaliraamene anatsalira ku Asiriya,monga mmene panali msewu waukulu woyendapo Israelipamene amachokera ku Igupto.