2Anthu a mitundu ina adzaperekeza a Israeliku dziko lawo.Tsono Aisraeli adzasandutsa anthu a mitundu ina ajakukhala antchito awo aamuna ndi aakazi mʼdziko la Yehova.Ndiye kuti Aisraeli adzasandutsa akapolo anthu amene kale anali ambuye awo.Iwo adzasandutsa akapolo anthu amene kale ankawalamulira ndi kuwazunza.
3Yehova akadzakupumitsani ku zowawa ndi mavuto, ndiponso kuntchito yakalavulagaga imene ankakugwiritsani,
4mudzayankhula monyogodola mfumu ya Babuloni kuti,
4Wopsinja uja watha!Ukali wake uja watha!
5Yehova wathyola chikwapu cha anthu oyipa,Iye waphwanya ndodo ya olamulira.
6Mfumu ya ku Babuloni inkakantha mitundu ya anthu mwaukalipowamenya kosalekeza,Iyo inkagonjetsa anthu a mitundu ina mwaukalindikuwazunza kosalekeza.
7Koma tsopano mayiko onse ali pa mpumulo ndi pa mtendere;ndipo akuyimba mokondwa.
8Ngakhale mitengo ya payini ndi mikungudza ya ku Lebanoniikuyimba za iwe mokondwa ndipo ikuti,“Chigwetsedwere chako pansi,palibe wina anabwera kudzatigwetsa.”
8
9Ku manda kwatekesekakuti akulandire ukamabwera;mizimu ya anthu akufa, aja amene anali atsogoleria dziko lapansi, yadzutsidwa.Onse amene anali mafumu a mitundu ya anthuayimiritsidwa pa mipando yawo.
10Onse adzayankha;adzanena kwa iwe kuti,“Iwenso watheratu mphamvu ngati ife;Iwe wafanana ndi ife.”
11Ulemerero wako wonse walowa mʼmanda,pamodzi ndi nyimbo za azeze ako;mphutsi zayalana pogona pakondipo chofunda chako ndi nyongolotsi.
11
12Wagwa pansi bwanji kuchoka kumwamba,iwe nthanda, mwana wa mʼbandakucha!Wagwetsedwa pansi pa dziko lapansi,Iwe amene unagonjetsapo mitundu ya anthu!
13Mu mtima mwako unkanena kuti,“Ndidzakwera mpaka kumwamba;ndidzakhazika mpando wanga waufumupamwamba pa nyenyezi za Mulungu;ndidzakhala pa mpando waufumu pa phiri losonkhanirako,pamwamba penipeni pa phiri la kumpoto.
14Ndidzakwera pamwamba pa mitambo;ndidzafanana ndi Wammwambamwamba.”
15Koma watsitsidwa mʼmandapansi penipeni pa dzenje.
15
16Anthu akufa adzakupenyetsetsanadzamalingalira za iwe nʼkumati,“Kodi uyu ndi munthu uja anagwedeza dziko lapansindi kunjenjemeretsa maufumu,
18Mafumu onse a mitundu ya anthu akugona mwaulemualiyense mʼmanda akeake.
19Koma iwe watayidwa kunja kwa manda ako,ngati nthambi yowola ndi yonyansa.Mtembo wako waphimbidwa ndi anthu ophedwa;amene anabayidwa ndi lupanga,anatsikira mʼdzenje lamiyalangati mtembo woponderezedwa.
20Zidzukulu za anthu oyipa sizidzakumbukika nʼpangʼono pomwe.
21Konzani malo woti muphere ana ake aamunachifukwa cha machimo a makolo awo;kuti angadzuke ndi kulanda dziko lapansindi kulidzaza dziko lonselo ndi mizinda yawo.
21
22Yehova Wamphamvuzonse akuti,“Ine ndidzathira nkhondo mzinda wa Babuloni.Ndidzachotseratu mu Babuloni dzina lake ndi onse otsaliramo.Ndiye kuti sipadzakhala ana kapena zidzukulu,”akutero Yehova.
23“Ndidzawusandutsa mzindawo malo okhalamo anungundiponso dambo lamatope;ndidzawusesa ndi tsache lowononga,”akutero Yehova Wamphamvuzonse.
25Ndidzawawononga Asiriya mʼdziko langa;ndidzawapondereza ndi mapazi pa mapiri anga;ndidzachotsa goli lawo pa anthu anga,ndipo ndidzachotsa katundu wawo pa mapewa awo.”
25
26Izi ndizo ndakonza kuti zichitike pa dziko lonse lapansi,ndatambasula dzanja pa anthu a mitundu yonse.
27Pakuti Yehova Wamphamvuzonse watsimikiza, ndipo ndani angamuletse?Dzanja lake latambasulidwa ndipo ndani angalibweze?
29Musakondwere inu Afilisti nonsekuti Asiriya amene anali ngati ndodo yokukanthani anathedwa;chifukwa kuchokera ku njoka yomweyi (mfumu ya Aasiriya) mudzatuluka mphiri,ndipo chipatso chake chidzakhala njoka yaliwiro ndiponso yaululu.
30Osaukitsitsa adzapeza chakudyandipo amphawi adzakhala mwamtendere.Koma anthu ako ndidzawawononga ndi njala,ndipo njalayo idzapha ngakhale opulumuka ako.
30
31Lirani kwambiri, anthu a pa chipata! Fuwulani kwambiri, anthu a mu mzinda!Njenjemerani ndi mantha, inu Afilisti nonse!Mtambo wa utsi ukuchokera kumpoto,ndipo palibe wamantha pakati pa ankhondo ake.
32Kodi tidzawayankha chiyaniamithenga a ku Filisitiya?“Yehova wakhazikitsa Ziyoni,ndipo mu mzinda wakewu, anthu ozunzika apeza populumukira.”