1Anthu a ku Mowabuatumiza mphatso za ana ankhosa onenepa,kuchokera ku Sela kudutsa chipululumpaka kukafika ku phiri la Ziyoni.
2Monga momwe mbalame zimawulukira uku ndi ukuakazimwaza mʼchisa,momwemonso akazi a ku Mowabuakuyendayenda ku madooko a Arinoni.
2
3Amowabu aja anawuza a ku Yuda kuti,“Tiwuzeni chochita, gamulani zoti tichite.Inu mutiteteze kwa adani anthu.Mukhale ngati mthunzi wathu dzuwa lili pa liwombo.Mutibise,musatipereke ife othawa nkhondo kwa adani athu.
4Lolani kuti anthu othawa nkhondo a ku Mowabu azikhala pakati panu;mukhale populumukira pawo kwa wowonongayo.”
5Mpando waufumu udzakhazikitsidwa mwachikondi;mmodzi mwa zidzukulu za Davide adzakhalapo mokhulupirika.Iyeyo poweruza adzatsata chilungamondipo adzalimbikitsa kuchita zachilungamo.
5
6Tinamva kuti Mowabu anadzikuza kwambiri.Kunyada kwawondi kunyogodola kwawo ndi kudzitama kwawo,zonse ndi zopanda phindu.
7Nʼchifukwa chake Amowabu akulira kwambiri;iwo akulirira dziko lawo.Akubuma momvetsa chisonichifukwa cha makeke a mphesa a ku Kiri Hareseti.
8Minda ya ku Hesiboni yauma,minda ya mpesa ya ku Sibina yaguga.Atsogoleri a mitundu ina anapondapondaminda ya mpesa wabwino,imene nthambi zake zinakafika ku Yazeri,mpaka kutambalalira ku chipululu.Mizu yake inakafikampaka ku tsidya la nyanja.
9Kotero Ine ndikulira, monga mmene akulirira anthu a ku Yazeri,chifukwa cha minda ya mpesa ya ku Sibima.Inu anthu a ku Hesiboni, inu anthu a ku Eleali,ndikukunyowetsani ndi misozi!Mwalephera kupeza zokolola,chifukwa cha nkhondo imene inawononga zokolola zonse.
10Chimwemwe ndi chisangalalo zalekeka ku minda yanu ya zipatso;palibe amene akuyimba kapena kufuwula mʼminda ya mpesa;palibe amene akupsinya vinyo ku malo opsinyira mphesa,pakuti ndathetsa kufuwula.
11Chifukwa chake moyo wanga ukulira ngati pangwe kulirira Mowabu,mtima wanga ukubuwula chifukwa cha Kiri Hareseti.
12Ngakhale anthu a ku Mowabuapite ku malo awo achipembedzokoma amangodzitopetsa ndi kutaya nthawi chabechifukwa sizidzatheka.
13Awa ndi mawu amene Yehova wayankhula kale zokhudza Mowabu.