1Uthenga wonena za Damasiko: “Taonani, mzinda wa Damasiko sudzakhalanso mzinda,koma udzasanduka bwinja.
2Mizinda ya Aroeri idzakhala yopanda anthundipo idzakhala ya ziweto, zimene zidzagona pansipopanda wina woziopseza.
3Ku Efereimu sikudzakhalanso linga,ndipo ku Damasiko sikudzakhalanso ufumu;Otsalira a ku Siriya adzachotsedwa ulemumonga anthu a ku Israeli,”akutero Yehova Wamphamvuzonse.
3
4“Tsiku limenelo ulemerero wa Yakobo udzazimirira;ndipo chuma chake chidzasanduka umphawi.
5Israeli adzakhala ngati munda wa tiriguumene anatsiriza kukolola.Adzakhalanso ngati munda wa mʼchigwa cha Refaimuanthu atatha kukunkha ngala za tirigu.
6Komabe Aisraeli ochepa okha ndiwo ati adzatsalemonga mʼmene zimatsalira zipatso ziwiri kapena zitatu pa nthambi ya pamwamba penipenikapena zipatso zisanu pa nthambi za mʼmunsimwa mtengo wa olivi akawugwedeza,”akutero Yehova, Mulungu wa Israeli.
6
7Tsiku limenelo anthu adzayangʼana Mlengi wawondipo adzatembenukira kwa Woyerayo wa Israeli.
8Iwo sadzakhulupiriranso maguwa ansembe,ntchito ya manja awo,ndipo sadzadaliranso mitengo ya mafano a Asera,ndiponso maguwa ofukizirapo lubani amene manja awo anapanga.
9Tsiku limenelo mizinda yawo yamphamvu, imene anasiya chifukwa cha Aisraeli, idzakhala ngati malo osiyidwa kuti awirire ndi kumera ziyangoyango. Ndipo yonse idzakhala mabwinja.
12Aa, mkokomo wa anthu a mitundu yambiri,akusokosa ngati kukokoma kwa nyanja!Aa, phokoso la anthu a mitundu ina,akusokosa ngati mkokomo wa madzi amphamvu!
13Ngakhale ankhondo a mitundu ina akubwera ndi mkokomo ngati wa madzi ambiri,koma adzathawira kutali Mulungu akadzawadzudzula.Yehova adzawapirikitsa ngati mankhusu owuluka ndi mphepo pa phiri,ndi ngati fumbi la kamvuluvulu asanayambe.