1Uthenga wonena za chipululu cha mʼmbali mwa Nyanja. Ankhondo a ku Elamu ndi Mediya adzabwera ngati kamvuluvulu amene akuwomba modutsa mʼmbali ya nyanja,kuchokera ku chipululu,dziko lochititsa mantha.
3Chifukwa cha zimenezi thupi langa likunjenjemera ndi mantha,ndikumva ululu ngati wa mayi amene akubereka;ndikuvutika kwambiri ndi zimene ndikumva,ndathedwa nzeru ndi zimene ndikuziona.
4Mtima wanga ukugunda,ndipo ndikunjenjemera ndi mantha;chisisira chimene ndakhala ndikuchifunachasanduka chinthu choopsa kwa ine.
4
5Ankhondo a ku Elamu ndi Mediya akukonza matebulo,akuyala mphasa,akudya komanso kumwa!Mwadzidzidzi anamva mawu akuti, “Dzukani inu ankhondo,pakani mafuta zishango zanu!”
6Zimene Ambuye akunena kwa ine ndi izi; “Pita, kayike mlondakuti azinena zimene akuziona.
7Taonani, anthu akubwera ali pa akavalondipo akuyenda awiriawiri,okwera pa bulukapena okwera pa ngamira,mlondayo akhale tcheru kwambiri.”
8Ndipo mlondayo anafuwula kuti, “Ambuye anga, tsiku ndi tsiku ndimakhala pa nsanja yolondera;Usiku uliwonse ndimakhala pa malo anga olondera.
9Taonani, uyo munthu akubwera atakwera pa galetaali ndi gulu la akavalo.Mmodzi wa iwo akuti,‘Babuloni wagwa, wagwa!Mafano onse a milungu yakeagwa pansi ndipo aphwanyika!’ ”
9
10Inu anthu anga opunthidwa ndi kupetedwa ngati tirigu,ine ndikukuwuzani zimene ndamvandikukuwuzani Uthenga wochokera kwa Yehova Wamphamvuzonse,Mulungu wa Israeli.
11Uthenga wonena za Duma: Munthu wina akundiyitana kuchokera ku Seiri kuti,“Iwe mlonda, usikuwu utha liti?Iwe mlonda, utha liti kodi usikuwu?”