1Uthenga wonena za Chigwa cha Masomphenya: Kodi chachitika nʼchiyani,kuti nonsenu mukwere pa madenga?
2Iwe mzinda wodzaza ndi chisangalalo chodzaza tsaya,iwe mzinda waphokoso ndi wosokonekera?Anthu ako ophedwa aja sanaphedwe ndi lupanga,kapena kufera pa nkhondo.
4Nʼchifukwa chake Ine ndinati, “Chokani pamaso panga;ndilekeni ndilire ndi mtima wowawa.Musayesere kunditonthozachifukwa cha kuwonongeka kwa anthu anga.”
4
5Lero Ambuye Yehova Wamphamvuzonse walola kuti tionemavuto ndi kugonjetsedwa ndiponso chisokonezomʼChigwa cha Masomphenya.Malinga agumuka,komanso anthu akanalira mofuwula ku mapiri.
6Ankhondo a ku Elamu anadza pa magaletandi akavalo ali ndi mivi mʼmanja.Ankhondo a ku Kiri anakonzeka ndi zishango.
7Zigwa zanu zachonde ndi zodzaza ndi magaleta,ndipo asilikali okwera pa akavalo ayikidwa pa zipata za mzinda;
9inu munaona kuti makoma ambiri a mzinda wa Davideanali ndi malo ambiri ogumuka;munasunga madzimu chidziwe chakumunsi.
10Munawerenga nyumba zonse za mu Yerusalemundipo munagwetsa nyumba zina kuti mulimbitse linga logumuka lija.
11Pakati pa makoma awiri munamanga chitsimechosungiramo madzi ochokera ku dziwe lakale,koma inu simunadalire Mulungu amene anapanga zimenezi,kapena kusamalako za Iye amene anazilenga kale lomwe.
13Koma mʼmalo mwake inu munakondwa ndi kusangalala;munapha ngʼombe ndi nkhosa;munadya nyama ndi kumwa vinyo.Inu mumati, “Tiyeni tidye ndi kumwapakuti mawa tifa!”
14Yehova Wamphamvuzonse wandiwululira mondinongʼoneza kuti, “Tchimo limeneli sindidzakhululuka mpaka tsiku la kufa kwanu,” akutero Ambuye, Yehova Wamphamvuzonse.
15Chimene Ambuye, Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Pita, ukanene kwa Sabina kapitawo,amene amayangʼanira nyumba yaufumu:
16Kodi ukuchita chiyani kuno, nanga ndani anakupatsa chilolezokuti udzikumbire manda kuno,kudzikumbira manda pa phirindi kudzisemera malo opumulira mʼthanthwe?
19Ine ndidzakuchotsa pa ukapitawo wakondipo ndidzakutsitsa pa udindo wako.
20“Tsiku limenelo ndidzayitanitsa mtumiki wanga, Eliyakimu mwana wa Hilikiya.
21Ndidzamuveka mkanjo wako ndi kumangira lamba wako mʼchiwuno mwake ndi kumupatsa ulamuliro wako. Iye adzakhala kholo la amene amakhala mu Yerusalemu ndiponso a fuko la Yuda.
22Ndidzamupatsa ulamuliro wa banja la Davide. Adzatsekula ndipo palibe adzatseke, adzatseka popanda wina kutsekula.
23Ufumu wake udzakhala wokhazikika ngati chikhomo chokhomedwa pa malo olimba. Anthu adzalemekeza nyumba ya abale ake chifukwa cha iye.
24Ana ndi abale a nyumba ya abambo ake adzakhala ngati katundu pa iye ngati ziwiya zopanda ntchito zimene zapachikidwa pa chikhomo.