1Uthenga wonena za Turo: Lirani mofuwula, inu oyendetsa sitima za pa madzi za ku Tarisisi:pakuti mzinda wa Turo wawonongedwandipo mulibe nyumba kapena dooko.Zimenezi anazimvapochokera ku Kitimu.
2Khalani chete inu anthu okhala mʼmbali mwa nyanja,inu amalonda a ku Sidoni,iwe amene unalemera ndi anthu oyenda pa nyanja.
3Pa nyanja zazikulupanabwera tirigu wa ku Sihori;zokolola za ku Nailo, ndipo munachita malondandi anthu a mitundu ina.
3
4Chita manyazi, iwe Sidimupakuti nyanja yayankhula, linga la ku nyanja (Turo) layankhula kuti,“Sindinamvepo zowawa za kubereka kapena kuberekapo mwana;sindinalerepo ana aamuna kapena kulera ana aakazi.”
5Mawuwa akadzamveka ku Igupto,iwo adzachita mantha akadzamva kuti Turo wawonongeka.
5
6Wolokerani ku Tarisisi,lirani mofuwula, inu anthu okhala mʼmbali mwa nyanja.
7Kodi uwu si mzinda wachisangalalo uja,mzinda wakalekale,umene anthu ake ankapitakukakhala ku mayiko akutali?
8Kodi ndani anakonza zimenezi kuti zigwere Turo, mzinda umene unakhazikitsa mizinda ina,mzinda umene amalonda ake ndi akalongandi otchukapa dziko lapansi?
9Yehova Wamphamvuzonse anakonza zimenezikuti athetse kunyada kwawondi kutsitsa anthu otchuka a pa dziko lapansi.
9
10Mubalalike mʼdziko mwanu ngati mtsinje wa Nailoinu anthu a ku Tarisisi,pakuti mulibenso chokutetezani.
11Yehova watambasula dzanja lake kuloza ku nyanjandipo wagwedeza maufumu ake.Iye walamula kuti Kanaaniagwetse malinga ake.
12Iye anati, “Simudzakondwanso konse,inu anthu opanikizidwa a ku Sidoni, tsopano wamphwanyidwa!
12“Ngakhale muwolokere ku Kitimu, kumeneko simukapezako mpumulo.”
13Onani dziko la Ababuloni,anthu amenewa tsopano atheratu!Asiriya asandutsa Turo kukhalamalo a zirombo za ku chipululu;anamanga nsanja zawo za nkhondo,anagumula malinga akendipo anawasandutsa bwinja.
13
14Lirani mofuwula, inu anthu oyendetsa sitima za pa madzi za ku Tarisisi;chifukwa malinga ako agwetsedwa!
15Pa nthawi imeneyo Turo adzayiwalika pa zaka 70, amene ndi masiku a moyo wa mfumu. Koma potsiriza pa zaka 70 zimenezi, Turo adzakhala ngati mkazi wachiwerewere woyimbidwa mu nyimbo:
17Pakutha pa zaka 70, Yehova adzachitapo kanthu pa Turo. Iye adzabwerera ku ntchito yake yakale monga mkazi wachiwerewere ndipo adzachita zachiwerewere ndi maufumu onse a dziko lapansi.
18Koma phindu lake ndi malipiro ake adzazipereka kwa Yehova; sadzazikundika kapena kuzisunga. Phindu lake lidzapita kwa mtumiki wa Yehova kuti agule zakudya zambiri ndi zovala zokongola.