13Zimenezi ndizo zidzachitikire mitundu yonse ya dziko lapansindiponso pakati pa mitundu ya anthu.Zidzakhala ngati pamene mitengo ya olivi yayoyoledwa,kapena ngati nthawi ya kunkha la mphesa atatsiriza kukolola.
13
14Koma otsala onse akufuwula ndi kuyimba mwachimwemwe;anthu akumadzulo akutamanda ukulu wa Yehova.
15Nʼchifukwa chake inu akummawa, tamandani Yehova;ndi inu okhala mʼmphepete mwa nyanja kwezani dzina la Yehova, Mulungu wa Israeli.
16Kuchokera kumalekezero a dziko lapansi tikumva kuyimba kotamanda“Wolungamayo.”
16Koma ine ndinati, “Ndatheratu, ndatheratu! Tsoka kwa ine!Anthu achinyengo akupitirizabe kuchita zachinyengo,inde chinyengo chawo chikunkerankera mʼtsogolo.”
23Mwezi udzanyazitsidwa, dzuwa lidzachita manyazi;pakuti Yehova Wamphamvuzonse adzakhala mfumu ndipo adzalamulira;pa Phiri la Ziyoni ndi ku Yerusalemu,ndipo adzaonetsa ulemerero wake pamaso pa akuluakulu.