2Inu mwasandutsa mzinda uja kukhala mulu wamiyala.Ndipo mzinda wamalinga wasanduka bwinja,linga la anthu achilendo lero si mzindansondipo sidzamangidwanso.
3Nʼchifukwa chake anthu amphamvu adzakulemekezani;mizinda ya mitundu ya anthu ankhanza idzakuopani.
4Inu mwakhala ngati populumukira pa anthu osauka,mwakhala ngati kobisalirako munthu wovutika pa nthawi ya masautso ake.Mwakhala ngati pobisalirapopa nthawi ya mphepo yamkuntho ndi mthunzi pa nthawi ya dzuwa.Pakuti anthu ankhanzaali ngati mphepo yamkuntho yowomba pa khoma,
5ndiponso ngati kutentha mʼdziko lowuma.Inu mumaletsa phokoso la anthu achilendo.Monga momwe mthunzi wa mtambo umachepetsa kutentha,inu munaletsa nyimbo za anthu ankhanza.
5
6Pa phiri ili Yehova Wamphamvuzonse adzakonzeraanthu a mitundu yonse madyerero a zakudya zokoma ndi vinyo wabwino.Phwando la nyama yononandi vinyo wabwino kwambiri.