8Yehova mwawalanga powapirikitsa ndi kuwatumiza ku ukapolo,mwawachotsa ndi mpweya wanu woopsa,monga zimachitikira pa tsiku la mkuntho wochokera kummawa.
9Yehova adzakhululuka kulakwa kwa Yakobo.Iwo adzaonetsa kuti alapadi pamene adzaphwanya miyala yonse ya guwa lachikunja,ngati mmene anthu amaphwanyira miyala yanjerezampaka kukhala ngati fumbi lokhalokha.Sipadzapezekanso mafano a Aserakapena maguwa ofukiza lubani.
10Mzinda wamalinga uja wasanduka bwinja,wasanduka malo osiyidwa, ndi kutayidwa ngati chipululu;kumeneko amadyetselako ana angʼombekumeneko zimapumulako ziwetondi kumwetula nthambi za mitengo kotheratu.
11Pamene nthambi za mitengoyo zauma, zimathyokandipo amayi amabwera nazitola ndi kuzisandutsa nkhuni.Pakuti awa ndi anthu opanda nzeru;kotero Mulungu amene anawapanga sadzachitira chisoni,ndipo Mlengi wawo sawakomera mtima.
12Tsiku limenelo Yehova adzasonkhanitsa pamodzi anthu ake mmodzimmodzi kumalo opunthira tirigu, kuchokera ku mtsinje wa Yufurate mpaka ku mtsinje wa ku Igupto.
13Ndipo tsiku limenelo lipenga lalikulu lidzalira. Amene akuzunzika ku Asiriya iwo amene ali ku ukapolo ku Igupto adzabwera ndi kudzalambira Yehova pa phiri lopatulika mu Yerusalemu.