1Tsoka ufumu wonyada wa zidakwa za ku Efereimu.Tsoka kwa ulemerero wake wokongola umene ukufota ngati duwalimene lili pa mutu pa anthuoledzera a mʼchigwa chachonde.
2Taonani, ambuye ali naye wina wamphamvu ndi nyonga.Iye adzabwera ngati mkuntho wamatalala ndi namondwe wowononga,ngati madzi amphamvu osefukira a mvula yamkuntho;ndipo adzawagwetsa pansi mwankhanza.
3Ulamuliro wa atsogoleri oledzeraa ku Efereimu adzawuthetsa.
4Ndipo ulemerero wokongola wa mzinda umene uli ngati duwalofota pamutu pa anthu oledzera a mʼchigwa chachonde uja,udzakhala ngati nkhuyu yoyambirira kupsaimene munthu akangoyiona amayithyolanthawi yokolola isanakwane.
6Iye adzapereka mtimawachilungamo kwa oweruza,adzakhala chilimbikitso kwaamene amabweza adani pa zipata za mzinda.
6
7Nawonso awa ali dzandidzandi chifukwa cha vinyondipo akusochera chifukwa cha mowa:ansembe ndi aneneri akudzandira chifukwa cha mowandipo akusokonezeka chifukwa cha vinyo;akusochera chifukwa cha mowa,akudzandira pamene akuona masomphenya,kupunthwa pamene akupereka chigamulo.
8Pa matebulo onse pali masanzi okhaokhandipo palibenso malo wopanda zonyansa.
8
9Iwo akuti, “Kodi munthu ameneyu akufuna aphunzitse ndani?Uthengawu akufuna kufotokozera yani?Ndi kwa ana amene aleka kuyamwa,kwa makanda ongowachotsa kumene ku bere?
10Akuyesa kumatiphunzitsa pangʼonopangʼonolemba ndi lemba, mzere ndi mzere,phunziro ndi phunziro.Zonsezi akungoti apa pangʼono apa pangʼono.”
10
11Mulungu adzayankhula kwa anthu ake kudzera mwa anthu aziyankhulo zachilendo, ziyankhulo zosamveka bwino.Mulungu adzayankhula kwa anthu awa, amene
12anakuwuzani kuti,“Malo opumulira ndi ano,otopa apumule, malo owusira ndi ano.”Koma inu simunamvere.
13Choncho Yehova adzakuphunzitsanipangʼonopangʼono lemba ndi lemba,mzere ndi mzere, phunziro ndi phunziro.Kotero mudzayenda ndi kugwa chambuyo,adzapweteka ndi kukodwa mu msamphandipo adzakutengani ku ukapolo.
13
14Nʼchifukwa chake imvani mawu a Yehova,inu anthu achipongwe amene mumalamulira anthu awa mu Yerusalemu.
15Inu mumayankhula monyada kuti, “Ife tinachita pangano ndi imfa,ife tachita mgwirizano ndi manda.Pamene mliri woopsa ukadzafikasudzatikhudza ife,chifukwa timadalira bodza ngati pothawirapo pathundi chinyengo ngati malo anthu obisalapo.”
16Tsono zimene Ambuye Yehova akunena ndi izi: “Taonani, ndikuyika mwala wovomerezeka ndi amisiringati maziko mu Ziyoni,mwala wapangodya, wamtengowapatali wopanga maziko amphamvu;munthu amene awukhulupirira sadzagwedezeka.
17Ntchito zolungama zidzakhala ngati chingwe choyezera maziko ake,ndipo chilungamo chidzakhala chowongolera mzere;matalala adzawononga malo anu othawirapo, amene ndi mabodza,ndipo madzi adzamiza malo anu obisalako.
18Pangano limene munachita ndi imfa lidzathetsedwa;mgwirizano wanu ndi manda udzachotsedwa.Pakuti mliri woopsa udzafika,ndipo udzakugonjetsani.
19Ndipo ukadzangofika udzakutengani.Udzafika mmawa uliwonse,usiku ndi usana.”
21Yehova adzamenya nkhondo monga anachitira ku phiri la Perazimuadzakalipa monga anachitira ku chigwa cha Gibiyoni;adzagwira ntchito yake yooneka ngati yachilendo,ndipo zimene ati adzachite zidzakhala ngati zodabwitsa.
25Pamene iye wasalaza mundawo,kodi samafesa mawere ndi chitowe?Kodi suja samadzala tirigundi barele mʼmizere yake,nadzala mchewere mʼphepete mwa mundawo?
26Mulungu wake amamulangizandi kumuphunzitsa njira yabwino.
26
27Mawere sapunthira chopunthira cha galeta lopanda mikombero,kapena chitowe sapuntha popondetsapo mikombero ya galeta;mawere amapuntha ndi ndodondipo chitowe amapuntha ndi kamtengo.