1Tsoka kwa iwe, Arieli, Arieli,mzinda umene Davide anakhazikitsamo zithando za nkhondo!Papite chaka chimodzi kapena ziwirindipo masiku a zikondwerero zanu azipitirirabe ndithu.
2Komatu Ine ndidzathira nkhondo Arielindipo kudzakhala kulira ndi kudandaula,mzindawo udzasanduka ngati ngʼanjo ya guwa lansembe.
3Ine ndidzamanga misasa ya nkhondo kulimbana ndi mzindawo;ndidzakuzungulira ndi nsanja za nkhondondi kumanga mitumbira yanga ya nkhondo kulimbana nawe.
4Utagwetsedwa pansi, iwe udzayankhula kuchokera mʼnthaka,mawu ako adzatuluka uli mʼfumbi,adzamveka ngati a mzukwa.Mawu ako adzamveka ngati onongʼona kuchokera mʼfumbi.
4
5Koma chigulu cha adani ako chidzasanduka chifwirimbwiti.Chigulu cha ankhondo achilendo chidzabalalika ngati mungu wowuluzika ndi mphepo.Mwadzidzidzi ndi mosayembekezereka,
6Yehova Wamphamvuzonse adzabwerandi mabingu ndi chivomerezi ndi phokoso lalikulu,kamvuluvulu ndi namondwe ndi malawi a moto wonyeketsa.
7Tsono chigulu chankhondo cha mitundu ina yonse chimene chikulimbana ndi mzinda wa Arielinʼkumathira nkhondo mzindawo, malinga ake ndi kuwuzinga,chigulu chonsecho chidzazimirira ngati maloto,gati zinthu zoziona mʼmasomphenya usiku.
8Chidzakhala ngati munthu wanjala wolota akudya,koma podzuka ali nayobe njala;kapena ngati munthu waludzu wolota akumwa,koma podzuka, ali nalobe ludzu, kummero kwake kuli gwaa.Izi zidzachitika pamene chigulu cha nkhondo cha mitundu ina yonsechikunthira nkhondo Phiri la Ziyoni.
8
9Pitirizani kuledzera ndipo mudzakhala opusa.Dzitsekeni mʼmaso ndipo mukhale osapenya,ledzerani, koma osati ndi vinyo,dzandirani, koma osati ndi mowa.
10Yehova wakugonetsani tulo tofa nato.Watseka maso anu, inu aneneri;waphimba mitu yanu, inu alosi.
11Kwa inu mawu onsewa ali ngati buku lotsekedwa, ndipo ngati lipatsidwa kwa wina wodziwa kuwerenga ndi kunena kuti, “Chonde tawerengani bukuli,” iye adzati, “Sindingathe popeza ndi lomatidwa.”
12Kapena ngati lipatsidwa kwa amene sadziwa kuwerenga ndi kunena kuti, “Chonde werenga bukuli,” iye adzayankha kuti, “Ine sindidziwa kuwerenga.”
13Ambuye akuti, “Anthu awa amandipembedza Ine ndi pakamwa pawo,ndi kundilemekeza Ine ndi milomo yawo,koma mitima yawo ili kutali ndi Ine.Kundipembedza kwawo ndi kwa chiphamaso.Amandipembedza motsata malamulo a anthu amene anaphunzitsidwa.
14Nʼchifukwa chakenso Ine ndidzapitirirakuwachitira ntchito zodabwitsa;nzeru za anthu anzeru zidzatha,luntha la anthu aluntha Ine ndidzalinyoza.”
15Tsoka kwa amene amayesetsakubisira Yehova maganizo awo,amene amachita ntchito zawo mu mdima nʼkumanena kuti,“Ndani amene akundiona kapena ndani akudziwa zimene ndikuchita?”
22Choncho Yehova amene anawombola Abrahamu, akunena kwa zidzukulu za Yakobo kuti, “Anthu anga sadzachitanso manyazi;nkhope zawo sizidzagwanso ndi manyazi.
23Akadzaona ana awo ndintchito ya manja anga pakati pawo,adzatamanda dzina langa loyera;adzazindikira kuyera kwa Woyerayo wa Yakobo,ndipo adzachita naye mantha Mulungu wa Israeli.