1Taonani tsopano, AmbuyeYehova Wamphamvuzonse,ali pafupi kuchotsa mu Yerusalemu ndi mu Yudazinthu pamodzi ndi thandizo;adzachotsa chakudya chonse ndi madzi onse,
2anthu amphamvu ndi asilikali ankhondo,oweruza ndi aneneri,anthu olosera ndi akuluakulu,
3atsogoleri a ankhondo makumi asanu ndi anthu olemekezeka,aphungu ndi anthu amatsenga ndi akatswiri pa za kulosera.
14Yehova akuwazenga milanduakuluakulu ndi atsogoleri a anthu ake:“Ndinu amene mwawononga munda wanga wa mpesa;nyumba zanu zadzaza ndi zolanda kwa amphawi.
16Yehova akunena kuti,“Akazi a ku Ziyoni ngodzikuza kwambiri,akuyenda atakweza makosi awo,akukopa amuna ndi maso awoakuyenda monyangʼamaakuliza zigwinjiri za mʼmiyendo yawo
17Nʼchifukwa chake Ambuye, adzatulutsa zipere pa mitu ya akazi a ku Ziyoniwo;Yehova adzachititsa dazi mitu yawo.”
18Tsiku limenelo Ambuye adzawachotsera zodzikongoletsera zawo: za mʼmiyendo, za ku mutu za mʼkhosi,
19ndolo ndi zibangiri, nsalu zophimba pa nkhope,
20maduku, zigwinjiri za mʼmiyendo ndi malamba, mabotolo a zonunkhira ndi zithumwa,
21mphete ndi zipini,
22zovala za pa mphwando, zipewa ndi mwinjiro, zikwama,
23magalasi oyangʼanira, zovala zosalala, nduwira ndiponso nsalu za mʼmapewa.
24Mʼmalo mwa kununkhira azidzanunkha,mʼmalo mwa lamba, adzavala chingwe;mʼmalo mwa tsitsi lopesa bwino, adzakhala ndi dazi;mʼmalo mwa zovala zabwino, adzavala chiguduli;mʼmalo mwa kunyadira kukongola adzachita manyazi.
25Iwe Yerusalemu anthu ako aamuna adzaphedwa ndi lupanga,asilikali ako adzafera ku nkhondo.
26Pa zipata za Ziyoni padzakhala kubuma ndi kulira;Iweyo udzasakazidwa nʼkukhala pansi, ukugubuduzika pa fumbi.