1Yehova akuti, “Tsoka kwa ana ondipandukiraamene amachita zowakomera iwo okha osati Ine,nachita mgwirizano wawowawokoma osati motsogozedwa ndi Ine.Choncho amanka nachimwirachimwira.
2Amapita ku Igupto kukapempha thandizokoma osandifunsa;amathawira kwa Farao kuti awateteze,ku Igupto amafuna malo opulumulira.
3Koma chitetezo cha Farao chidzakhala manyazi anu,malo a mthunzi a ku Igupto mudzachita nawo manyazi.
4Ngakhale kuti nduna zawo zili ku Zowani,ndipo akazembe awo afika kale ku Hanesi,
5aliyense wa ku Yuda adzachita manyazichifukwa cha anthu opanda nawo phindu,amene sabweretsa thandizo kapena phindu,koma manyazi ndi mnyozo.”
6Uthenga wonena za nyama za ku Negevi: Akazembe akuyenda mʼdziko lovuta ndi losautsa,mʼmene muli mikango yayimuna ndi yayikazi,mphiri ndi njoka zaululu.Iwo amasenzetsa abulu ndi ngamira chuma chawo,kupita nazo kwa mtundu wa anthuumene sungawathandize.
7Amapita ku Igupto amene thandizo lake ndi lachabechabe.Nʼchifukwa chake dzikolo ndalitchaRahabe chirombo cholobodoka.
24Ngʼombe ndi abulu amene amalima mʼmunda adzadya chakudya chamchere, chopetedwa ndi foloko ndi fosholo.
25Pa tsiku limene adani anu adzaphedwa ndi nsanja zawo kugwa, mitsinje ya madzi idzayenda pa phiri lililonse lalikulu ndi pa phiri lililonse lalingʼono.
26Mwezi udzawala ngati dzuwa, ndipo kuwala kwa dzuwa kudzawonjezereka kasanu nʼkawiri, ngati kuwala kwa tsiku limodzi. Yehova adzamanga mabala a anthu ake ndi kupoletsa zilonda zimene Iye anachititsa polanga anthu ake.
27Taonani, Yehova akubwera kuchokera kutali,ndipo mkwiyo wake ndiwonyeka ndi chiweruzo chake chidzakhala chopweteka.Iye wayankhula mwaukali kwambiri,ndipo mawu ake ali ngati moto wonyeka.
28Mpweya wake uli ngati mtsinje wosefukira,wa madzi ofika mʼkhosi.Iye adzasefa anthu a mitundu ina ndi sefa wosakaza;Iye akuyika zitsulo mʼkamwa mwa anthu a mitundu ina ngati akavalo,kuti ziwasocheretse.
29Ndipo inu mudzayimbamokondwa monga mumachitira usiku pa chikondwerero chopatulika.Mudzasangalalangati anthu oyimba zitoliropopita ku phiri la Yehova,thanthwe la Israeli.
30Anthu adzamva liwu la ulemerero la Yehovandipo adzaona dzanja lake likutsika pa iwondi mkwiyo woopsa, pamodzi ndi moto wonyeketsa,mphenzi, namondwe ndi matalala.
31Asiriya adzaopa liwu la Yehova,ndipo Iye adzawakantha ndi ndodo.
32Yehova akamadzalanga adani ake ndi ndodo,anthu ake adzakhala akuvina nyimbozoyimbira matambolini ndi azeze,Yehova ndiye ati adzamenyane ndi Asiriyawo.
33Malo otenthera zinthu akonzedwa kale;anakonzera mfumu ya ku Asiriya.Dzenje la motolo ndi lozama ndi lalikulu,ndipo muli nkhuni zambiri;mpweya wa Yehova,wangati mtsinje wa sulufule,udzayatsa motowo pa nkhunizo.