1Tsoka kwa amene amapita ku Igupto kukapempha chithandizo,amene amadalira akavalo,nakhulupirira kuchuluka kwa magaleta awo ankhondondiponso mphamvu za asilikali awo okwera pa akavalo,koma sakhulupirira Woyerayo wa Israeli,kapena kupempha chithandizo kwa Yehova.
2Komatu Yehovayo ndi wanzeru ndipo angathe kuwononga,ndipo sasintha chimene wanena.Adzalimbana ndi anthu ochita zoyipa,komanso ndi amene amathandiza anthu ochita zoyipa.
4Zimene Yehova akunena kwa ine ndi izi: “Monga mkango kapena msona wamkango umabangulaukagwira nyama yake,ndipo suopsedwa kapena kusokonezekandi kufuwula kwa abusa amene akulimbana nayo,momwemonso palibe chingaletseYehova Wamphamvuzonsekubwera kudzatchinjirizaphiri la Ziyoni ndi zitunda zake.
5Monga mbalame zowuluka pamwamba pa zisa zake,Yehova Wamphamvuzonse adzatchinjiriza Yerusalemu;ndi kumupulumutsa,iye adzawupitirira ndi kuwulanditsa.”
6Inu Aisraeli, bwererani kwa Iye amene munamuwukira kwakukulu.
7Pakuti tsiku limenelo nonsenu mudzataya mafano anu a siliva ndi golide amene mumapanga ndi manja anu auchimo.
8“Aasiriya adzaphedwa ku nkhondo ndi mphamvu osati za munthu.Lupanga, osati la munthu, lidzawawononga.Adzathawa ku nkhondo ndipo anyamata awoadzagwira ntchito yathangata.
9Mfumu yawo idzamwalira ndi mantha,ndipo atsogoleri awo ankhondo adzathawa ndi manthakusiya pambuyo mbendera yawo ya nkhondo.”Akutero Yehova, amene moto wake uli mu Ziyoni,ndipo ngʼanjo yake ili mu Yerusalemu.