1Tsoka kwa iwe, iwe wowonongawe,amene sunawonongedwepo!Tsoka kwa iwe, iwe mthirakuwiri,iwe amene sunanyengedwepo!Iwe ukadzaleka kuwononga,udzawonongedwa,ukadzasiya umʼthirakuwiri, adzakuwononga,ndipo ukadzaleka kuchita zachinyengo adzakunyenga.
2Inu Yehova, mutikomere mtima ife;tikulakalaka Inu.Tsiku ndi tsiku mutitchinjirize ndi mkono wanu,ndipo mutipulumutse pa nthawi ya masautso.
3Mukatulutsa liwu lanu longa bingu mitundu ya anthu imathawa;pamene Inu mwadzambatuka mitundu ya anthu imabalalika.
4Zofunkha za ku nkhondo za mitundu ina Aisraeli adzazisonkhanitsa ngati mmene limachitira dzombe.Iwo adzalumphira zofunkhazo monga mmene limachitira dzombe.
4
5Yehova wakwezeka kwambiri pakuti amakhala pamwamba pa zonseadzadzaza Ziyoni ndi chilungamo ndi chipulumutso.
6Iye adzakupatsani mtendere pa nthawi yanu,adzakupatsani chipulumutso chochuluka, nzeru zambiri ndi chidziwitso chochuluka;kuopa Yehova ngati madalitso.
8Mʼmisewu yayikulu mulibe anthu,mʼmisewu mulibe anthu a paulendo.Mdaniyo ndi wosasunga pangano.Iye amanyoza mboni.Palibe kulemekezana.
9Dziko likulira ndipo likunka likutha.Nkhalango ya Lebanoni ikuchita manyazi, yafota.Chigwa cha chonde cha Saroni chasanduka chachidalala.Masamba a mitengo ya ku Basani ndi Karimeli akuyoyoka.
19Simudzawaonanso anthu odzikuza aja,anthu aja achiyankhulo chosadziwika,chachilendo ndi chosamveka.
19
20Taonani Ziyoni, mzinda wa zikondwerero zachipembedzo chathu;maso anu adzaona Yerusalemu,mzinda wamtendere, tenti imene sidzachotsedwa,zikhomo zake sizidzazulidwa,kapena zingwe zake kuduka.
21Kumeneko Yehova adzaonetsa ulemerero wakendipo mzindawo udzakhala kasupe wa mitsinje yayikulu.Ngalawa za zopalasa sizidzapitamo,sitima zapamadzi zikuluzikulu sizidzayendamo.