1Chipululu ndi dziko lopanda madzi zidzasangalala;dziko lowuma lidzakondwandi kuchita maluwa.
2Dzikolo lidzakhala ndi maluwa ochulukalidzasangalala kwambiri ndi kufuwula mwachimwemwe.Lidzakhala ndi ulemerero monga wa ku mapiri a ku Lebanoni,maonekedwe ake wokongola adzakhala ngati a ku Karimeli ndi a ku Saroni.
2Aliyense adzaona ulemerero wa Yehova, ukulu wa Mulungu wathu.
3Limbitsani manja ofowoka,limbitsani mawondo agwedegwede;
4nenani kwa a mitima yamantha kuti;“Limbani mtima, musachite mantha;Mulungu wanu akubwera,akubwera kudzalipsira;ndi kudzabwezera chilango adani anu;akubwera kudzakupulumutsani.”
4
5Pamenepo maso a anthu osaona adzapenyansondipo makutu a anthu osamva adzatsekuka.
10Iwo amene Yehova anawawombola adzabwerera.Adzalowa mu mzinda wa Ziyoni akuyimba;kumeneko adzakondwa mpaka muyaya.Adzakutidwa ndi chisangalalo ndi chimwemwe,ndipo chisoni ndi kudandaula zidzatheratu.