5“Pita kwa Hezekiya ndipo ukamuwuze kuti, ‘Yehova, Mulungu wa kholo lake Davide akuti: Ndamva pemphero lako ndipo misozi yako ndayiona; ndidzakuwonjezera zaka 15 pa moyo wako.
6Ndipo ndidzakupulumutsa, iwe pamodzi ndi mzindawu mʼdzanja la mfumu ya ku Asiriya, Ine ndidzawuteteza mzindawu.
7“ ‘Ichi ndi chizindikiro cha Yehova kwa iwe kutsimikiza kuti Yehova adzachita zimene walonjeza:
8Chithunzithunzi chimene dzuwa likuchititsa pa makwerero a Ahazi ndidzachibweza mʼmbuyo makwerero khumi.’ ” Ndipo chithunzithunzi chinabwerera mʼmbuyo makwerero khumi.
9Ndakatulo ya Hezekiya mfumu ya ku Yuda imene analemba atadwala ndi kuchira:
10Ine ndinaganiza kutindidzapita ku dziko la akufapamene moyo ukukoma.
11Ndinaganiza kuti, “Sindidzaonanso Yehova,mʼdziko la anthu amoyo,sindidzaonanso mtundu wa anthukapena kukhala pamodzi ndi amene amakhala pa dziko lapansi lino.
12Nyumba yanga yasasukandipo yachotsedwa.Ngati tenti ya mʼbusa mwapindapinda moyo wanga,ngati munthu wowomba nsalu;kuyambira usana mpaka usiku mwakhala mukundisiya.
15Koma ine ndinganene chiyani?Yehova wayankhula nane, ndipo Iye ndiye wachita zimenezi.Chifukwa cha kuwawa kwa mtima wanga,ine ndidzayenda modzichepetsa masiku amoyo wanga onse.
16Ambuye, masiku anga ali mʼmanja mwanu.Mzimu wanga upeza moyo mwa Inu.Munandichiritsa ndikundikhalitsa ndi moyo.
17Ndithudi, ine ndinamva zowawa zoterekuti ndikhale ndi moyo;Inu munandisungakuti ndisapite ku dzenje la chiwonongekochifukwa mwakhululukiramachimo anga onse.
18Pakuti akumanda sangathe kukutamandani,akufa sangayimbe nyimbo yokutamandani.Iwo amene akutsikira ku dzenjesangakukhulupirireni.
19Amoyo, amoyo okha ndiwo amakutamandani,monga mmene ndikuchitira ine lero lino;abambo amawuza ana awo zakukhulupirika kwanu.
19
20Yehova watipulumutsa.Tiyeni tiyimbe ndi zoyimbira za zingwemasiku onse a moyo wathumʼNyumba ya Yehova.