2Ayankhuleni moleza mtima anthu a ku Yerusalemundipo muwawuzitsekuti nthawi ya ukapolo wawo yatha,tchimo lawo lakhululukidwa.Ndawalanga mokwanirachifukwa cha machimo awo onse.
2
3Mawu a wofuwula mʼchipululu akuti,“Konzani njira ya Yehovamʼchipululu;wongolani njira zake;msewu owongoka wa Mulungu wathu mʼdziko lopanda kanthu.
7Udzu umanyala ndipo maluwa amafotachifukwa cha kuwomba kwa mpweya wa Yehova.”Mawu aja anatinso, “Ndithudi anthu sasiyana ndi udzu.
8Udzu umanyala ndipo maluwa amafota,koma mawu a Mulungu wathu adzakhalapo mpaka muyaya.”
8
9Iwe amene ukulengeza nkhani yabwino ku Ziyoni,kwera pa phiri lalitali.Iwe amene ukulengeza nkhani yabwino ku Yerusalemu,fuwula kwambiri,kweza mawu, usachite mantha;uza mizinda ya ku Yuda kuti,“Mulungu wanu akubwera!”
10Taonani, Ambuye Yehova akubwera mwamphamvu,ndipo dzanja lake likulamulira,taonani akubwera ndi mphotho yakewatsogoza zofunkha zako za ku nkhondo.
11Iye adzasamalira nkhosa zake ngati mʼbusa:Iye adzasonkhanitsa ana ankhosa aakazi mʼmanja mwakendipo Iye akuwanyamula pachifuwa chakendi kutsogolera bwinobwino nkhosa zoyamwitsa.
11
12Kodi ndani akhoza kuyeza kuchuluka kwa madzi a mʼnyanja ndi chikhatho chake,kapena kuyeza kutalika kwa mlengalenga ndi dzanja lake?Ndani akhoza kuyeza dothi lonse la dziko lapansi mʼdengu,kapena kuyeza kulemera kwamapiri ndi zitunda ndi pasikelo?
13Ndani anapereka malangizo kwa Mzimu wa Yehovakapena kumuphunzitsa Iye monga phungu wake?
14Kodi Yehova anapemphapo nzeru kwa yani kuti akhale wopenya,kapena kuti aphunzire njira yoyenera ndi nzeru?Iye anapempha nzeru kwa yanindi njira ya kumvetsa zinthu?
14
15Ndithudi mitundu ya anthu ili ngati dontho la madzi ochoka mu mtsuko.Iwo akungoyesedwa ngati fumbi chabe pa sikelo;mʼmanja mwa Yehova zilumba nʼzopepuka ngati fumbi.
16Nkhalango ya ku Lebanoni singakwanire nkhuni zosonkhera moto pa guwa lansembe,ngakhale nyama zake sizingakwanire kupereka nsembe zopsereza.
17Pamaso pa Yehova mitundu yonse ya anthu ili ngati chinthu chopandapake;Iye amayiwerengera ngati chinthu chopanda phindundi cha chabechabe.
17
18Kodi tsono Mulungu mungamuyerekeze ndi yani?Kodi mungamufanizire ndi chiyani?
19Likakhala fano, mʼmisiri ndiye analipangandipo mʼmisiri wa golide amalikuta ndi golidenaliveka mkanda wasiliva.
25Woyera uja akuti, “Kodi mudzandiyerekeza Ine ndi yani?Kapena kodi alipo wofanana nane?”
26Tayangʼanani mlengalenga ndipo onani.Kodi ndani analenga zonsezi mukuzionazi?Yehova ndiye amene amazitsogolera ngati gulu la ankhondo,nayitana iliyonse ndi dzina lake.Ndipo popeza Iye ali ndi nyonga zambiri,palibe ndi imodzi yomwe imene inasowapo.