4Ndani anachita zimenezi ndi kuzitsiriza,si uja amene anayambitsa mitundu ya anthu?Ine Yehova, ndine chiyambindipo potsiriza pake ndidzakhalapo.”
4
5Mayiko amʼmbali mwa nyanja aona zimenezi ndipo akuopa;anthu a ku mathero a dziko lapansi akunjenjemera.Akuyandikira pafupi, akubwera;
6aliyense akuthandiza mnzakendipo akuwuza mʼbale wake kuti, “Limba mtima!”
7Mʼmisiri wa matabwa amalimbikitsa mʼmisiri wa golide,ndipo iye amene amasalaza fano ndi nyundoamalimbikitsa amene amalisanja pa chipala.Ponena za kuwotcherera iye amati, “Zili bwino.”Iye amalikhomerera fanolo ndi misomali kuti lisagwe.
7
8“Koma Iwe Israeli mtumiki wanga,Yakobo amene ndakusankha,Ndiwe chidzukulu cha Abrahamu bwenzi langa.
9Ndinakutengani kuchokera ku mapeto a dziko lapansi,ndinakuyitanani kuchokera ku mbali za kutali za dziko lapansi.Ine ndinati, ‘Iwe ndiwe mtumiki wanga;’Ndinakusankha ndipo sindinakutaye.
10Tsono usaope, pakuti Ine ndili nawe;usataye mtima chifukwa Ine ndine Mulungu wako.Ndidzakupatsa mphamvu ndipo ndidzakuthandiza,ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.
13Pakuti Ine Yehova, ndine Mulungu wako,amene ndikukugwira dzanja lako lamanjandipo ndikuti, usaope;ndidzakuthandiza.
14Usachite mantha, iwe Yakobo wofowoka ngati nyongolotsi,iwe wochepa mphamvu Israeli,chifukwa Ine ndidzakuthandiza,”akutero Yehova Mpulumutsi wako, Woyerayo wa Israeli.
15“Taona, ndidzakusandutsa ngati chipangizo chopunthira tiriguchatsopano, chakunthwa ndi cha mano ambiri.Udzanyenya mapiri ndi kuwaphwanyaphwanya,ndipo zitunda adzazisandutsa ngati mankhusu.
16Udzawapeta ndipo adzawuluka ndi mphepo komansoadzamwazika ndi kamvuluvulu.Koma iwe udzakondwera chifukwa Ine ndine Mulungu wako,ndipo udzanyadira chifukwa cha Ine Woyerayo wa Israeli:
16
17“Pamene amphawi ndi osauka akufunafuna madzi,koma sakuwapeza;ndipo kummero kwawo kwawuma ndi ludzu.Ine Yehova ndidzayankha pemphero lawo;Ine, Mulungu wa Israeli, sindidzawasiya.
18Ndidzayendetsa mitsinje mʼmalo owuma,ndi akasupe adzatumphuka mu zigwa.Ndidzasandutsa chipululu kukhala dziwe la madzindipo dziko lowuma kukhala akasupe a madzi.
19Mʼchipululu ndidzameretsamkungudza, kasiya mchisu ndi mtengo wa Olivi.Mʼdziko lowuma ndidzaza mitengoya payini, ya mkuyu ndi ya mlombwa,
20kuti anthu aone ndi kudziwa;inde, alingalire ndi kumvetsa,kuti Yehova ndiye wachita zimenezi;kuti Woyera wa Israeli ndiye anakonza zimenezi.
20
21“Yehova akuwuza milungu ina kuti, ‘Fotokozani mlandu wanu.’Mfumu ya Yakobo ikuti, ‘Perekani umboni wanu.’