4sadzafowoka kapena kukhumudwampaka atakhazikitsa chilungamo pa dziko lapansi,ndi mpaka mayiko a mʼmbali mwa nyanja atafika poyembekezera malangizo ake.”
4
5Yehova Mulunguamene analenga zamlengalenga ndi kuziyalika,amene analenga dziko lapansi ndi zonse zimene zimabereka,amenenso amapereka mpweya kwa anthu ake okhala mʼdzikomo,ndi moyo kwa onse oyendamo, akuti,
6“Ine Yehova, ndakuyitana chifukwa Ine ndine wolungama;ndikugwira dzanja ndipondidzakuteteza.Ndakupereka kukhala pangano langa kwa anthundi kuwunika kwa anthu a mitundu ina.
7Udzatsekula maso a anthu osaona,udzamasula anthu a mʼndendendi kutulutsa mʼndende anthu okhala mu mdima.
7
8“Ine ndine Yehova: dzina langa ndi limenelo!Sindidzapereka ulemerero wanga kwa wina aliyensekapena matamando anga kwa mafano.
19Ali wosaona ndani, si mtumiki wanga kodi?Ndipo ndani ali wosamva ngati mthenga amene ndamutuma?Kodi ndani ali wosaona ngati uja ndinachita naye pangano,kapena wosaona ndani ngati mtumiki wa Yehova?
20Iwe waona zinthu zambiri, koma sunazisamale;makutu ako ndi otsekuka koma sumva kanthu.”
21Chinamukomera Yehovachifukwa cha chilungamo chake,kapena lamulo lake kukhala lalikulu ndi lopambana.