1Yehova akuti, “Mvera tsopano, iwe Yakobo, mtumiki wanga,Israeli, amene ndinakusankha.
2Yehovaamene anakupanga iwe, anakuwumba iwe mʼmimba ya amayi ako,ndi amene adzakuthandiza iwe. Iye akuti,Usachite mantha, iwe Yakobo, mtumiki wanga,Yesuruni, amene ndinakusankha.
3Pakuti ndidzathira madzi pa nthaka yowuma,ndi kuyendetsa mitsinje mʼdziko lowuma;ndidzatumiza Mzimu wanga pa ana anu,ndi kutsitsa madalitso anga pa zidzukulu zanu.
4Iwo adzakula ngati udzu wothirira bwinondi ngati bango lomera mʼmbali mwa mitsinje ya madzi oyenda.
5Wina adzanena kuti, ‘Ine ndine wa Yehova;’wina adzadzitcha yekha wa banja la Yakobo;winanso adzalemba pa dzanja lake, ‘Wa Yehova’ndipo adzadzitcha wa banja la Israeli.
6“Yehova Mfumundi Mpulumutsi wa Israeli, Yehova Wamphamvuzonse akuti:Ine ndine woyamba ndi wotsiriza;palibenso Mulungu wina koma Ine ndekha.
10Ndani amasema mulungu ndi kuwumba fano,limene silingamupindulire?
11Iye pamodzi ndi anzake onse adzawachititsa manyazi;amisiri a mafano ndi anthu chabe.Aloleni onse asonkhane ndi kuyima pabwalo la milandu;onse adzaopsedwa ndipo adzachita manyazi.
11
12Mmisiri wa zitsulo amatenga chitsulondipo amachiyika pa makala amoto;ndi dzanja lake lamphamvuamachisula pochimenya ndi nyundo.Pambuyo pake mʼmisiri uja amamva njala natha mphamvu;iye samwa madzi, ndipo amalefuka.
13Mmisiri wa matabwa nayenso amayeza mtengo ndi chingwendipo amajambula chithunzi ndi cholembera;amasema bwinobwino ndi chipangizo chakendipo amachiwongola bwino ndi chida chake.Amachipanga ngati munthu,munthu wake wokongolakuti aliyike mʼnyumba yake yachipembedzo.
14Amagwetsa mitengo ya mkungudza,mwinanso amatenga mtengo wa payini kapena wa thundunʼkudzisankhira mtengo wabwino pakati pa mitengo ya mʼnkhalango,ndipo amadzala mtengo wa payini ndi kuwuleka kuti ukule ndi mvula.
15Mitengoyo munthu amachitako nkhuni;nthambi zina amasonkhera moto wowotha,amakolezera moto wophikira buledindi mbali ina ya mtengowo amapangira mulungu ndipo amapembedza;iye amapanga fano ndi kumaligwadira.
16Chigawo china cha mtengowo amasonkhera motowowotcherapo nyama imeneamadya, nakhuta.Iye amawotha motowo ndipo amanena kuti,“Aa! Ndikumva kutentha; pano pali moto.”
17Chigawo chotsala amapanga kamulungu, fano lake limenelo;amaligwadira ndi kulipembedza.Amapemphera kwa fanolo ndipo amanena kuti,“Iwe ndiwe mulungu wanga, ndipulumutse.”
18Anthu otere sadziwa kanthu, samvetsa kanthu kalikonse;maso awo ndi omatirira ndipo sangathe kuona,ndipo mitu yawo ndi yogontha kotero sangathe kumvetsa.
19Palibe amene amayima nʼkulingalira.Palibe wanzeru kapena womvetsa zinthu bwino woti nʼkunena kuti,chigawo china cha mtengowo ndinasonkhera moto;pa makala ake ndinaphikira buledi,ndinawotchapo nyama ndipo ndinadya.Chigawo chotsalachi ndipangire chinthu chonyansachi.Kodi ndidzagwadira mtengo?
20Munthu wotere ali ngati wodya phulusa, maganizo ake opusa amusocheretsa;motero kuti sangathe kudzipulumutsa yekha kapena kudzifunsa kuti,“Kodi chinthu chili mʼmanja mwangachi si chabodza?”