1Yehova akuyankhula ndi wodzozedwa wakeKoresi amene anamugwira dzanja lamanjakuti agonjetse mitundu ya anthundi kuwalanda mafumu zida zawo zankhondo,ndi kutsekula zitsekokuti zipatazo zisadzatsekedwenso ndi ichi:
2Ine ndidzayenda patsogolo pako,ndi kusalaza mapiri;ndidzaphwanya zitseko za mkuwandi kuthyola mipiringidzo ya chitsulo.
3Ndidzakupatsa chuma chobisika mu mdima,katundu wa pamalo obisika,kotero kuti udziwe kuti Ine ndine YehovaMulungu wa Israeli, amene ndakuyitana pokutchula dzina.
4Chifukwa cha mtumiki wanga Yakobo,chifukwa cha wosankhidwa wanga Israeli,Ine ndakuyitana pokutchula dzinandipo ndakupatsa dzina laulemungakhale iwe sukundidziwa Ine.
5Ine ndine Yehova ndipo palibenso wina;kupatula Ine palibenso Mulungu wina.Ndidzakupatsa mphamvu,ngakhale sukundidziwa Ine,
6kotero kuti kuchokera kummawa mpaka kumadzuloanthu adzadziwa kuti palibe wina koma Ine ndekha.Ine ndine Yehova,ndipo palibenso wina.
7Ndimalenga kuwala ndi mdima,ndimabweretsa madalitso ndi tsoka;ndine Yehova, amene ndimachita zonsezi.
11“YehovaWoyerayo wa Israeli, ndiponso Mlengi wake akunena,zokhudza zinthu zimene zikubwera ndi izi:Kodi iwe ukundifunsa za ana anga,kapena kundilamula pa zokhudza ntchito zanga?
12Ndine amene ndinapanga dziko lapansindikulenga munthu kuti akhalemo.Ine ndi manja anga ndinayalika thambo;ndimalamulira zolengedwa zonse za mlengalenga.
13Ndine amene ndidzawutsa Koresi kuti chilungamo changa chikwaniritsidwe:ndipo ndidzawongolera njira zake zonse.Iye adzamanganso mzinda wangandi kumasula anthu anga amene ali mu ukapolo,wopanda kupereka ndalama kapena mphotho,akutero Yehova Wamphamvuzonse.”
14Yehova akuti, “Chuma cha ku Igupto ndi chuma cha malonda cha Kusi chidzakhala chanu.Anthu amphamvu zawo ndi athanzi a ku Sebaadzabwera kwa inundipo adzakhala anthu anu;iwo adzidzakutsatani pambuyo panuali mʼmaunyolo.Adzakugwadiranindi kukupemphani, ponena kuti,‘Ndithudi Mulungu ali ndi inu, ndipo palibenso wina;palibenso mulungu wina.’ ”
15Zoonadi inu muli ndi Mulungu wobisikaamene ali Mulungu ndi Mpulumutsi wa Israeli.
16Onse amene amapanga mafano adzawachititsa manyazi ndi kuwanyozetsa.Adzakhala osokonezeka maganizo.
19Ine sindinayankhule mwachinsinsi,pamalo ena a mdima;Ine sindinaziwuze zidzukulu za Yakobo kuti,“Ndifunefuneni ku malo kopanda kanthu.”Ine Yehova, ndimayankhula zoona;ndikunena zolungama.
19
20Yehova akuti, “Sonkhanani pamodzi ndipo mubwere;yandikirani, inu amene munapulumuka pothawa nkhondo kwa anthu a mitundu ina.Ndinu opanda nzeru amene mumanyamula mafano a mitengo,amene mumapemphera kwa milungu imene singathe kupulumutsa.
21Fotokozani mlandu wanu,mupatsane nzeru nonse pamodzi.Kodi ndani ananeneratu zimenezi kalekale?Ndani anazifotokozeratu zimenezi nthawi yamakedzana?Kodi si Ineyo Yehova?Ndipo palibenso Mulungu wina kupatula Ine,Mulungu wolungama ndi Wopulumutsa,palibenso wina kupatula Ine.
21
22“Tembenukirani kwa Ine kuti mupulumuke,inu anthu onse a pa dziko lapansi,pakuti Ine ndine Mulungu ndipo palibenso wina.
24Iwo adzanene kwa Ine kuti,‘Chilungamo ndi mphamvu zimapezeka mwa Yehova yekha.’ ”Onse amene anamuwukira Iyeadzabwera kwa Iye ndipo adzachita manyazi.
25Koma mwa Yehova zidzukulu zonse za Israelizidzapambana ndi kupeza ulemerero.