1Beli wagwada pansi, Nebo wawerama;nyama zonyamula katundu za nyamula milungu yawo.Mafano awo asanduka katundu wolemera pa msana pa ngʼombe.Asandukadi ngati katundu pa msana pa nyama zotopa.
2Nyamazo zikuwerama ndi kufuna kugwa ndi milunguyo;sizikutha kupulumutsa katunduyo,izo zomwe zikupita ku ukapolo.
3Mverani Ine, Inu nyumba ya Yakobo,inu nonse otsala a mʼnyumba ya Israeli,Ine ndakhala ndi kukusamalirani kuyambira mʼmimba ya amayi anu,ndakhala ndikukunyamulani chibadwire chanu.
4Mpaka pamene mudzakalambe ndi kumera imvindidzakusamalirani ndithu.Ndinakulengani ndipo ndidzakunyamulani,ndidzakusamalirani ndi kukulanditsani.
4
5“Kodi inu mudzandifanizira ndi yani, kapena mufananitsa ndi yani?Kodi mudzandiyerekeza kapena kundifanizitsa ndi yani?