8“Ndipo tsopano, tamvera, iwe wongokonda zokondweretsawe,amene ukukhala mosatekesekawe,umaganiza mu mtima mwako kuti,‘Ine ndi Ine, ndipo kupatula ine palibenso wina.Sindidzakhala konse mkazi wamasiye,ndipo ana anga sadzamwalira.’
9Koma mʼkamphindi, ndiponso tsiku limodzi,zinthu ziwiri izi zidzakuchitikira:ana ako kukufera komanso kukhala mkazi wamasiye.Zimenezi zidzakuchitikira kwathunthungakhale ali ndi amatsenga ambirindi mawula amphamvu.
10Iwe unkadalira kuyipa kwakondipo unati, ‘Palibe amene akundiona.’Kuchenjera ndi nzeru zako zidzakusokoneza,choncho ukuganiza mu mtima mwako kuti,‘Ine ndine basi, ndipo kupatula ine palibenso wina.’
11Ngozi yayikulu idzakugwerandipo sudzadziwa momwe ungayipewere ndi matsenga ako.Mavuto adzakugwerandipo sudzatha kuwachotsa;chipasupasu chimene iwe sukuchidziwachidzakugwera mwadzidzidzi.
13Malangizo onse amene unalandira angokutopetsa basi!Abwere patsogolopa anthu amene amatanthauzira za kumwamba kuti adzakupulumutseni.Abwere amene amayangʼana nyenyezi, ndi kumalosera mwezi ndi mwezizimene ziti zidzakuchitikire.
14Ndithudi, anthuwo ali ngati phesi;adzapsa ndi moto.Sangathe kudzipulumutsa okhaku mphamvu ya malawi a moto.Awa si makala a moto woti wina nʼkuwotha;kapena moto woti wina nʼkuwukhalira pafupi.
15Umu ndi mmene adzachitire amatsenga,anthu amene wakhala ukugwira nawo ntchitondi kuchita nawo malonda chiyambire cha ubwana wako.Onse adzamwazika ndi mantha,sipadzakhala ndi mmodzi yemwe wokupulumutsa.”